MkwasoNkhani Zina

Akupindula ndi ulimi wa nthochi ku Ntcheu

Wolemba: Joseph KAYIRA

Nthawi zambiri ukakhala   mtsogoleri, kaya ndi pamudzi, kaya ndi pa kampani, anthu amayembekezera zambiri kuchokera kwa iwe. Umayenera kukhala mtsogoleri wa chikondi, wamasomphenya komanso wochita zimene ukulangiza anthu amene ukuwatsogolera aja. Ngati ndiwe mfumu, ufumu wako umalemekezeka kapena kulemerera ngati pakhomo pako palinso pa chitsanzo. Izitu ndi zomwe akuchita a Gulupu Harold Mwenye, kwa Senzani m’boma la Ntcheu.

Mfumuyi, yomwe ili pansi pa Mfumu Yaikulu Tsikulamowa, ku Ntcheu imakangalika kwambiri pa nkhani zaulimi komanso zosamalira chilengedwe. Mafumu amene ali pansi pake nawo amachilimika pa nkhani ya ulimi komanso yoonetsetsa kuti anthu sakuononga chilengedwe kaamba koti ziwirizi zimayendera limodzi. A Gulupu a Mwenye alinso ndi nkhalango yosiriritsa ku Likudzi yomwe imawathandiza mu njira zosiyanasiyana.

Koma pano mfumuyi yati yayamba ulimi wa nthochi, womwe ena amene ayeserapo kale, akupi-ndula nawo kwambiri. Iyo yati anthu ambiri amaganiza kuti nthochi zimachita bwino ku Thyolo ndi ku Mulanje kokha, koma nthochi zimachita bwino paliponse, kuphatikizapo ku Ntcheu.

“Pano ndayamba ulimi wa nthochi. Mudabwa kuti koma ulimi umenewu ku Ntcheu ungatheke? Inde. Ulimi uliwonse ndi wotheka bola kutsatira malangizo omwe alangizi a zaulimi akunena. Kuno ku Ntcheu timalima pafupifupi mbewu iliyonse, nchifukwa chake inenso ndinaganiza zoyamba kulima nthochi. Mu nthochi muli ndalama.

“Kuti ndiyambe kulima nthochi ndinachita chidwi ndi munthu wina yemwe amadzafuna malo olima kumudzi kwathuku. Munthuyo atapatsidwa malo anadula mitengo ndikuyamba kulima nthochi. Kwa ife zinali zachilendo chifukwa tinazolowera kulima chimanga ndi mbewu zina. Koma munthuyu atayamba kukolola nthochi tonse tinali odabwa ndi kuchuluka kwa nthochi yomwe amakagulitsa ku Blantyre,” anatero a Gulupu a Mwenye.

Iwo akuti galimoto la munthuyo limafika kumundako, womwe uli m’mbali mwa mtsinje wa Lisungwi, m’mudzi mwa a Mfumu a Funsani, mwina kawiri pa sabata, kudzatuta nthochi. Kumeneko mlimiyu anadzala ntchochi pafupifupi 4,000. Izi zinachititsa kuti nayo mfumuyi iganize zoyamba kulima nthochi. 

Gulupu Mwenye akuti anachita chiganizo choyamba kulima ntchochi zaka zinayi zapitazo. Atatero anakagula mbewu ya nthochi 700 nkudzadzala pa munda wa pa nyumba yawo m’mbali mwa msewu wa Blantyre-Lilongwe pa Senzani. Iwo amati akuchita moyesa koma patatha masiku, nthochiyo inagwira modabwitsa.

“Pakali pano ndili mkati mo-gulitsa ntchochiyo ndipo mkoko umodzi umatha kufika K30,000 kapena kuposera apo. Anthu ambiri abizinesi akumadzaoda ntchochi kwa ine. Maganizo omati nthochi kuti uyipeze koma upite ku Thyolo akuchedwetsa anthu. Taonani ine ndikuchita zodabwita pa ekala imodzi,” anatero a Gulupu a Mwenye.

Gulupu Mwenye: Ndinachita chidwi ndi ulimiwu nditaona munda wa munthu wina (Chithunzi: Joseph Kayira)

Iwo afotokozanso kuti athandizapo kale alimi ambiri ku Likudzi powagawira mbewu ya nthochi kuti nawo akaone poyambira. Cholinga cha mfumuyi ndi choti anthu ake ambiri ayambenso kulima nthochi kuti azipha ma-kwacha komanso akatero azitha kuthandizika pa zosowa zawo pakhomo.

“Chimene ndikufuna ndi choti anthu ayambe kuchita ulimi monga umenewu chifukwa ndiwosavuta. Mabanja amene angalimbikire azapeza phindu ndikutukula miyoyo yawo. Maganizo amene ndili nawo ndiwoti alimi abwere pamodzi nkupanga magulu a alimi a nthochi kuti potero azitha kuthandizika mosavuta,” anatero a Gulupu a Mwenye.

Ulimi wa nthochi wawa-thandiza kuti loto loti alumikize magetsi nyumba yawo litheke mwamsanga. Komanso phindu lomwe akupeza ku malonda a nthochi lawathandiza kuti kugula zipangizo za ulimi monga fetereza, mankhwala ndi zina, ziphweke.

Iwo ati pakali pano, akukwanitsa kumawonjezera minda ina kaamba koti mphamvu zilipo – maka ku mbali ya chuma chomwe chikuchokera mu nthochi.

Maloto awo ena ndi woti akufuna kuti akumbe chitsime chomwe chizithandiza kuti akwanitse ulimi wanthirira wa nthochi, akaonjezera minda ina. Iwo akuti cholinga chokhala ndi chitsimechi nkuti chithandize alimi ena amene awonetsa kale chidwi chokhala mu koparetivu kapena kalabu kuti azichitira ulimi wawo ndi malonda awo pamodzi.

“Anthu akufuna kwabwino – ku boma, mabungwe, makampani ndi ena – atati atithandiza ndi chitsime ndiye kuti ulimi wathu udzapita patsogolo kwambiri. Monga m’mene boma limatilimbikitsira, cholinga cha ulimi wathu ndi kufuna kuthetsa umphawi kuyambira pakhomo. Misika ya nthochi ndiyambiri; mitengonso imapereka chilimbikiso.

“Alimi a nthochi atati achuluka komanso madzi akupezeka chaka chonse, mudzaona kuti ku Ntcheu kudzakhala ngati ku Thyolo kumene pa nkhani yotulutsa nthochi. Kuthekera kulipo ndithu koma chofunika ndi kuwathandiza alimi a nthochi ndi zowayenereza kuti azitulutsa ntchochi yambiri,” anatero a Gulupu a Mwenye.

A Gulupu a Mwenye akuti mphwayi sizimanga mtolo ndipo akulangiza anthu amene sanapangebe chiganizo pa za ulimi wa nthochi mdera lawo kuti asapitirire kutaya nthawi kaamba koti akusemphana ndi galimoto ya malipiro.

“Chuma chili mthaka; chuma chili mu nthochi,” akutero a Gulupu a Mwenye.