Uncategorized

Amangidwa ataba pa famu

Malingana ndi m’neneri wa polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, oganiziridwawa ndi George Watson, wa zaka 25; Dikilani Chokazinga, wa 29; Richard Lyton, wa zaka 40, Positani Gediyasi, wa zaka 32; Samuel Banda, wa zaka 27; ndi Chibvumbulutso Banda, wa zaka 30.

Iwo ati anthuwa anaba majenereta awiri, ma pampu atatu, tanki ya madzi, zipangizo za mphamvu yadzuwa zitatu, ndi zipangizo zamagetsi ndi zina.

A Chigalu ati malingana ndi mwini famuyi, yemwe sitimutchula dzina lake, iye anawuza apolisiwa kuti upanduwu unachitika pakati mwezi wa Ogasiti 2024 ndi Januwale 2025 kwa Njewa.

Omwe anachita izi samadziwika mpaka nthawi yomwe apolisi anayamba kuchita kafukufuku wawo. Ndipo atawamanga anthuwa anawalondolera apolisiwa komwe anagulitsa katunduyu komwe anapeza zipangizo za mphamvu ya dzuwa, mapaipi, zitseko za chitsulo ndi zina. Ndipo apolisiwa akuchita chotheka kuti apeze katundu wina wotsala yemwe anabedwayu.

Anthuwa akawonekera ku bwalo la milandu sabata yamawa komwe akayankhe mlandu wakuba.

Watson amachokera m’mudzi mwa Kanyoza Village, Mfumu yayikulu Ganya, m’boma la Ntcheu; Chokazinga, Lyton, Gediyasi, ndi Chivumbulutso Banda amachokera m’mudzi mwa Ching’amba, Mfumu yayikulu Njewa, ndipo Samuel Banda amachokera mudzi mwa Kalolo, Mfumu yayikulu Kalolo ku Lilongwe.


#Montfortmedianews