MkwasoUncategorized

Ansembe amanga nyumba yogona ophunzira

Wolemba: Monique MARCO, Mtolankhani Wapadera

Bungwe la ansembe achibadwiri mu dayosizi ya Mangochi lati limanga nyumba yogonamo ophunzira pa sukulu yapamwamba ya DMI m’boma la Mangochi ngati njira imodzi yopeza ndalama zothandizira ansembewa akadwala.

M’mbuyomu ansembe mu dayosiziyi akhala akuvutika kupeza chisamaliro chabwino cha mankhwala ndipo amalephera kupita m’zipatala zabwino akadwala kaamba kosowa ndalama.

Wapampando wa ansembe achibadwiri m’dayosiziyi Bambo Augustine Friday anati akonza njira zosiyanasiyana kuti apeze ndalama zokwana K15 miliyoni zomangira nyumbayi.

Ambuye Stima: Ithandiza ansembewa

“Padakali pano tili ndi nyumba imodzi imene tinamanga ku DMI imene imatipatsa ndalama yocheperako chifukwa choti ndalamayi timailandira kawiri pachaka. Tinachiona chofunika kwambiri kuti timangenso nyumba ina,” anatero Bambo Friday.

Iwo anapitiriza kuti anthu ena akufuna kwabwino alonjeza kuti athandiza  kupereka ndalama kuti malingalirowa atheke.

Bambo Friday anati Phungu wa Nyumba ya Malamulo wa m’dera la kummwera chakuzambwe kwa boma la Mangochi a Shadrick Namalomba, ali patsogolo kumema anthu ena akufuna kwabwino kuti athandize pa ntchitoyi.

Posachedwapa dayosiziyi inachititsa mpikisano wamwayi ndi wamwayi ku St Augustine Cathedral pomwe anthu ena adalonjezanso kuthandizanso ndi ndalama.

“Abalewa analonjeza kutithandiza ndi matumba a simenti komanso ena ndi ndalama. Tikalandira katundu ameneyu kuphatikizira ndalama zimene tinatolera pa mpikisano wa wamwayi ndi wamwayiwu, ntchitoyi tiyiyambapo. Tikupitiriza kupempha enanso akufuna kwabwino kuti apitirize kutithandiza ndi cholinga choti nyumbayi ithe mwamsanga,” anapitiriza Bambo Friday.

A Namalomba, omwe analonjeza kuthandiza ndi matumba 100 a simenti, anati anachiona chofunika kupempha amzawo ena kuti athandizepo kuti cholinga cha anse-mbewa chitheke.

Iwo anaulula kuti anthu ena alo-njeza kuthandizapo. Iwo anati Phungu wa Nyumba ya Malamulo, yomwenso ndi nduna ya zachuma a Joseph Mwanamvekha alonjeza ndalama yokwana K500,000 ndipo Dr Thom Mpinganjira, yemwe ndi mkulu wa FDH Bank alonjeza ndi matumba 100 a simenti.

Anthu ena amene alonjeza ndi a James Chuma (matumba a simenti 75), mkulu wa Malawi Bureau of Standards a Simon Mandala alonjeza K500,000 komanso a Patrick Liphava alonjeza matumba (24). Kampani ya Print Arts and Supplies yalonjeza matumba a simenti khumi.

Episikopi wa dayosiziyi Ambuye Montfort Stima anati nyumbayi ithandiza ansembe omwe alipowa komanso ena obwera kutsogolo  chifukwa “idzakhalapo mpaka kalekale ikuthandiza ansembewa.”

2 thoughts on “Ansembe amanga nyumba yogona ophunzira

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *