Apolisi achenjeza zotengera lamulo m’manja
Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA
Komishonalawa Polisi Arlene Baluwa am’chigawo chakummawa apempha anthu m’dziko muno kuti asamatengere lamulo m’manja mwawo pakachitika zinthu.
A Baluwa anayankhula izi pamene anakumana ndi mafumu ndi achitetezo akumudzi kutsatira ziwawa zomwe zinachitika ku Chilipa m’boma la Mangochi zomwe zinachititsa kuti ofesi ya polisi iwonongedwe.
“Zomwe achita anthu powononga ofesi ya polisi chifukwa choti anapulumutsa munthu yemwe amamume-nya ndizosaloledwa ndipo ndi kuphwanya malamulo,” anatero a Baluwa.
A Baluwa anati udindo wa polisi ndi kuteteza anthu ndi katundu ndipo zomwe anachita apolisiwa ndi zololedwa komanso kutsata malamulo ndipo samayenera kuwapanga chipongwe.
Iwo anadzudzula mchitidwewu kuti ndi woipa komanso apolisi afufuza zomwe zinachitika ndipo omwe akukhudzidwa lamulo lidzagwira ntchito mosakondera.
Malinga ndi Mfumu Yayikulu Chilipa, akazi awo a Bongo Nanumbwa adamwalira ndipo bamboyu amapemphedwa kuti azisamala ana awo. Izi sizinasangalatse akuchikazi omwe amanena kuti mkuluyu ndi mfiti.
“Nkhaniyi anayitengera kubwalo kwa Gulupu Bwanado. Mkati mokambirana zinthu zinafika poyipa anthu akumudziwo anayamba kumumenya mkuluyu,” inatero mfumu Chilipa.
Kutsatira mkanganowu apolisi adayitanidwa kuti akapulumutse mkuluyu yemwe anamutsekela m’chitokosi pomuteteza. Zimenezi sizinasangalatse anthuwa omwe anamemana ndi kukagenda polisi mpaka kuwonongeka komanso ku-yatsa moto malo omwe amadikilira asanamutulutse woganiziridwayo m’chitokosi. Woganiziridwayo anavulazidwa ndi anthuwa chifukwa anamugenda ndi miyala.
Mfumu Chilipa yati ndi yokhumudwa ndi mchitidwewu ndipo ina-tsimikizira apolisi kuti ofesi yawo ikonzedwanso chifukwa sangakhale opanda achitetezo m’derali.
Wofalitsa nkhani zapolisi m’chigawo chakummawa a Joseph Sauka anati padakali pano oganiziridwawa akulandira thandizo kuchipatala chaching’ono cha Chilipa ndipo apolisi atsegula kale milandu iwiri, wovulaza munthu mwadala komanso wowononga katundu.