Bungwe la Abambo mu mpingo wa Katolika liyendera ndende ya Mangochi
Wolemba: Joseph KAYIRA
Bungwe la Abambo [Catholic Men Organisation – CMO] mu mpingo wa Katolika masiku apitawa lapereka katundu wosiyanasiyana kwa akaidi omwe ali pandende ya Mangochi. Bungweli lomwe alikhazikitsa posachedwapa mu Dayosizi ya Mangochi lati zina mwa zolinga zomwe analikhazikitsira ndi kuthandiza osauka ndi ocheperekedwa monga akundende.
Malingana ndi mtsogoleri [Chaplain] wa gululi, Bambo Paul Lapozo, ati bungweli linakayendera aku ndende kaamba koti anthuwa amakumana ndi mavuto ambiri.
“Pambali polimbikitsana ngati Bungwe la Abambo pa mapemphero komanso kutumikira mpingo mu njira zosiyanasiyana, bungwe linachiona cha mtengo wapatali kukayendera anzathu aku ndende ya Mangochi komwe tinakagawana nawo zosiyanasiyana. Tinakagawana nawo katundu monga nyemba, soya pieces, mafuta ophikira, shuga, mabuku a nyimbo za mpingo wa Katolika ndi makorona,” anatero Bambo Lapozo.
Bambo Lapozo anati bungweli linakawayendera andendewa pa 18 Epulo ngati njira imodzi yokagawana nawo mawu ndi katundu mu nyengo yokumbukira kuuka kwa Ambuye Yesu. Iwo anapemphanso anthu akufuna kwabwino kuti achite zomwe linachita gulu la CMO poyendera andende, omwe kawirikawiri amaiwalidwa.
“Muona kuti munthu akapita ku ndende amatha kuiwalidwa komanso pena anthu akaona munthu ali ndende amaona ngati ndiye wolakwitsitsa. Zimenezi anzathu amene ali kundende zimawadandaulitsa; anatifotokozera kuti ena ali kumeneko chifukwa sanathe kudziteteza pa khoti osati chifukwa analakwira lamulo. Kuwayendera anthuwa ndi kukawapatsa kenakake kumawapatsa chiyembekezo,” anatero Bambo Lapozo.
Bungweli layala mapologalamu osiyanasiyana monga kuyenda [big walk] ndi cholinga chofuna kupeza ndalama zothandira anthu osauka ndi ovutika.
“Tikhala tikuchita zimenezi ndi cholinga chothandiza anzathu amene akuvutika m’makwalalamu. Pali ambiri omwe amasowa ngakhale sopo, chakudya ndi zovala. Onsewa tikufuna titawafikira. Koma kuti izi zitheke nafe tisowa anthu akufuna kwabwino kuti athandize Bungwe la Abambo,” iwo anatero.
Bambo Lapozo ati akufuna kuti Bungwe la Abambo lisefukire pena paliponse mu Dayosizi ya Mangochi ndi cholinga choti mamembala ake azitha kutumikira mpingo kudzera m’maluso awo osiyanasiyana.
“Pali aambo ambiri amene ali ndi luso lomwe likhoza kuthandiza kumanga mpingo wodzidalira. Mu mpingo muli amakaniko, makalipentala, mabilidala ndi ena ambiri. Onsewa akhoza kuchita zodabwitsa pa parishi yawo. Tikufuna mpingo udziwagwiritsa ntchito abambo amenewa potero nkudzamitsa mpingo wodzidalira,” anatero Bambo Lapozo.
Bungweli likufunanso kuthandiza abambo kukhala umoyo wodzidalira pa chuma, kutumikira mpingo dni kutenga mbali pa zitukuko zosiyanasiyana m’maparishi awo. M’mbuyomu ndi bungwe la amayi la Catholic Women Organisation (CWO) lomwe lakhala likutumikira kwambiri. Bambo Lapozo ati abambonso ali ndi kuthekera kotumikira mpingo monga m’mene amayi akuchitira.