CHAKA MU BOMA LA TONSE
Patatha chaka chilowereni m’boma mgwirizano wa Tonse, womwe ndi wa zipani zisanu ndi zinai, akatswiri pa ndale ndiulamuliro wabwino ati zikuonetsa kuti boma la Pulezidenti Lazarus Chakwera layamba bwino pa zambiri ngakhale kuti malonjezano ena sanakwaniritsidwebe.
Zipani za Malawi Congress (MCP) ndi UTM ndi zomwe zikutsogolera mgwirizanowu ndipo zinalowa m’boma kutsatira chisankho chatsopano
chomwe khoti lianalamula kuti chichitike pa 23 Juni chaka chatha. Izi zinachitika kaamba ka chigamulo cha khoti lapadera lomwe linati chisankho cha pulezidenti chomwe chinachitika mu mwezi wa Meyi 2019chinali ndi zolakwika zambiri.Malingana ndi katswiri pankhani zandale a Ernest Thindwa, kwakukulu boma la Tonse layamba bwino chifukwa labweretsa kusintha pa kayendetsedwe ka zinthu. Mwachitsanzo, iwo anati bomali lawonetsa kuti ndi mdani wa katangale komanso kuwonesetsakuti kagwiridwe ka ntchito m’boma ndikapamwamba komanso kaukadaulo. A Thindwa, womwe ndi mphunzitsi ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor, anatinso pali kusakondera pa nkhani ya kasankhidwe ka anthu m’maudindo ofunikira kwambiri. “Boma la Tonse kwakulu lachita wino. Mutha kuwona kuti
aliyense amene ali ndizomuyenereza akupatsidwa mwayi m’maudindo akulu akulu. Izi zilinso chimodzimodzi pa kasankhidwe ka nduna za boma,” anatero a Thindwa Iwo anapitiriza kunena kuti bomali lachitanso bwino kwambiri pokonza ubale ndi maiko oyandikana nawo a
Tanzania ndi Mozambique. Katswiriyu anatinso bomali likulemekeza kwambiri maufulu a anthu posamawaopseza komanso kumamenya anthu mwachisawawa monga m’mene zinaliri ndi boma la chipani cha Democratic Progressive (DPP). Koma iwo anati kumbali ina, utsogoleri wa bomali ukumaonetsa kufooka pakuchita chiganizo. Iwo anati Pulezidenti Chakwera nthawi zina satha kusunga zomwe walonjeza.
Pamenepa anatchula za kusintha nduna za boma. A Thindwa anapempha bomali kuti liyesetse kutukula mizinda ya m’dziko muno. “Anthu akungozimangira nyumba mwachisawawa. Nyumba zina zomwe zili m’mizinda yathu sizikuyenera kukhalamo. Pakuyenera kukhala dongosolo labwino bwino,” iwo anatero. A Billy Mayaya, omwe ndi m’modzi wa akuluakulu aku bungwe lomenyera maufulu anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) anati boma la mgwirizano wa Tonse likuyesetsa kuchita zakupsa poyerekeza ndi zomwe linkachita
boma la DPP. A Mayaya ati pa nkhani yolimbana ndi katangale, boma la mgwirizano wa Tonse likuyesetsa kuti chuma cha boma chisapitirire
kusakazika. “Chiwerengero chochuluka cha milandu yokhudza katangale ndi chizindikiro kuti nkhondo yothana ndi katangale ikuyenda bwino. Komabe Amalawi akufuna onse amene adaba ndalama za boma ndipo milandu yawo ili ku khoti iyende mwa changu ndi kufika
kumapeto. Amene apezeke wolakwa apite ku ndende. “Komanso kusankhidwa kwa mayi Martha Chizuma kukhala mkulu wa bungwe lolimbana ndi katangale la Anti-Corruption Bureau, ndi chitsimikizo kuti boma la mgwirizano wa Tonse likufunadi kuthana ndi mchitidwe wa katangalem’dziko muno,” anatero a Mayaya. A Mayaya ayamikiranso boma la mgwirizano wa Tonse kaamba ka momwe layendetsera
bwino ndondomeko yogulira zipangizo za zaulimi zotsika mtengo ya Affordable InputsProgramme (AIP) yomwe yathandiza kuti dziko la Malawi likolore zakumunda, maka chimanga, zochuluka Iwo alangizanso boma kuti lichite machawi pa nkhani ya ulimi wa fodya kaamba koti
mbewuyi ili pachiopsezo. A Mayaya ati popeza boma limadalira kwambiri mbewu ya fodya popeza ndalama zakunja, boma la mgwirizano wa Tonse likhale pansi ndi kupeza chomwe chingalowe m’malo mwa fodya kuti chuma chipitirire kupita patsogolo. Boma la mgwirizano wa Tonse lidalonjezanso kudzalemba ntchito achinyamata 1 miliyoni koma mpaka pano izi sizinachitike. A Mayaya atiboma lichite chotheka kuti kampeni yolemba achinyamata ntchito ipindulire Amalawi. “Mwa zina, boma liphunzitse achinyamata ntchito zamanja kudzera m’makoleji
osiyanasiyana. Izi zingathandize achinyamata kukhala odziyimira paokha. Ntchito isangokhla yolembedwa mmaofesi ayi. “Komanso pokhala Malawi ndi dziko longotukuka kumene, nkofunikanso kuika chidwi pa ntchito zamafakitale,” atero a Mayaya. Mwa zina, a Mayaya ati
boma la mgwirizo wa Tonse liunikenso malonjezano ake ndi kuonetsetsa kuti likuchita zomwe linalonjeza.