MkwasoUncategorized

Spear’ Mbandambanda wati ‘sanathe’

Mbandambanda: Sindinasiye kuimba

Wolemba: Bartholomew BOAZ

Pamene anthu ambiri amaganiza zoti Enort ‘Spear’ Mbanda-mbanda, yemwe adatchuka ndi nyimbo ya ‘Kuchimwa Kulibe Mwini’ wapachika magitala, iye wabwera poyera kuulula kuti “sanathe” ndipo akubwera ndi chimbale chatsopano.

Mbandambanda adatulutsa ‘Kuchimwa Kulibe Mwini’ m’chaka cha 1998 ndipo adatulutsapo zimbale zina monga ‘Ndapita’ komanso ‘Mwaonjeza’.

“Ndinakhala chete kwa kanthawi inde koma sikuti ndinasiya kuimba. Ndakhala ndikukonza nyimbo zimene pano ndakonzeka kudzitulutsa.

Anthu ayembekezere nyimbo zabwino chifukwa chimbale chimenechi chikhala chakupsa bwino,” anatero Mbandambanda.

Iye wati chimbale chatsopanochi mutu wake ndi ‘Mau a Ambuye’ ndipo akuchijambulitsa ku malo ojambulira nyimbo womwe mwini wake ndi Coss Chiwalo. M’chimbalechi ati muli nyimbo monga ‘Kusunga Mwambo’, ‘Kalekale’, ‘Kwathu’, ‘Okondedwa’,  ‘Musamamenyane’, ‘Ndife Bukhu’ ndi ‘Uchembere Wanu Amayi’ ndipo wadziimba kwenikweni mu zamba za rhumba, reggae ndi chikhalidwe.

Koma Mbandambanda wape-mpha anthu akufuna kwabwino kuti amuthandize kuwombola chimbalechi kuti chifike pa msika msanga. Iye wati akusowa ndalama yokwana K150,000 yokha kuti awombole chimbalechi ku situdiyo.

“Coss akundijambula pango-ngole poonera ndimmene nyimbo zangazo ziliri ndipo wandipatsa mwayi woti ndilipire pambuyo pa zonse. Amene angafune kundithandiza atha kulumikizana nane pa nambala iyi 0999494935,” watero Mbandambanda.

Padakali pano Mbandambanda akumaimba mu kwaya ya Montfort Media momwe mulinso mkhalakale yemwe amakanyanga nsambo mu bandi ya Alleluya, Foster Chimangafisi.