MkwasoUncategorized

Kajoke wadzivulira yekha chisoti

Kajoke (Kumanja) kulandira nkhuku kuchokera kwa sapota

Wolemba: Victor SINGANO Junior, Mtolankhani Wapadera

Katswiri wosewera kutsogolo mu timu ya Nyasa Big Bullets Hassan Kajoke wati akudzivulira yekha chipewa pokhala mmodzi mwa anyamata amene amalimbirana nawo pomwetsa zigoli mu ligi yayikulu ya TNM.

Iye wati ngakhale walephera kutenga mphoto yomwetsa zigoli zambiri sakudandaula kwambiri ndipo wafunira zabwino zonse katswiri wa Silver Strikers Khuda Muyaba potenga mphotoyi.

Muyaba, yemwe wamwetsa zi-goli zokwana 21 analumirana mano pa mpikisano womwetsa zigoli ndi Kajoke komanso katswiri wa Be Forward Wanderers Babatunde Adepoju. Ndipo Kajoke, yemwe anachokera ku timu yaying’ono ya Bullets kumayambiriro a chaka chatha ndipo kunali kusewera kwake koyamba mu ligi yayikulu, anamwetsa zigoli 16.

“Sindikumva kuwawa kulikonse monga mukudziwa kuti chinali chaka changa choyamba mu ligiyi ndipo chinali chaka chophunzira momwe umakhalira mpira mu ligiyi. Komabe ndikumadzivulira ndekha chisoti pokwanitsa kumwetsa zigoli zonsezi chifukwa sizinali zophweka. Panopa ndingofunira zabwino Khuda potenga mphotoyi,” anatero Kajoke.

Iye anati ayesetsa kuchilimika kuti akonze zolakwika zomwe anali nazo kuti adzathe kutenga mphotoyi chaka chino.

“Ndaona zolakwika zanga ndipo ndikudziwanso kuti aphunzitsi anga aona ndipo ayesetsa kundikonza kuti ndikhale bwino kuposa momwe ndinaliri chaka chatha. Ndithokozenso akuluakulu onse pondikhulupirira kuti ndizimenya pafupipafupi. Sizinali zapafupi potengera kuti ku timu kwathu tili ndi osewera ena omwe ndi othekera komanso acha-mbakale,” anatero Kajoke.