‘CHIGAMULO SIMATHERO A DZIKO’
Wolemba: Joseph KAYIRA ndi Rose Chipumphula CHALIRA
Pamene anthu akudikira zotsatira za ku khoti lamamulo (Constitutional Court) pa mlandu umene chipani cha UTM ndi mtsogoleri wake a Dr Saulos Chilima komanso a Malawi Congress (MCP) ndi mtsogoleri wake a Dr Lazarus Chakwera anakasuma kuti chisankho cha pulezidenti chichitikenso, Amalawi apemphedwa kusunga bata komanso kuti chigamulocho simathero a zonse ndipo moyo ukuyenera kupitirira popanda ziwawa komanso kusaononga katundu wa boma ndi mabizinesi.
Masiku apitawa, a Chakwera pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe anapempha anthu kuti akhale bata komanso adzavomereze zomwe khoti lingazagamule. Pa chisankho cha pulezidenti, bungwe loyendetsa zisankho mu dziko muno lidalengeza kuti a Peter Mutharika a chipani cha Democratic Progressive (DPP) ndiwo adapambana. Wotsatira anali a Chakwera kenako pa nambala 3 panali a Chilima.
Khoti la zamalamulo lakhala likumva nkhaniyi kwa miyezi isanu ndi itatu ndipo anthu ali ndi mantha kuti mwina pakhoza kudzakhala zipolowe khoti likalengeza chigamulo chake chomwe akuti chikhoza kutuluka pasanadutse pa 3 Febuluwale chaka chino.
A Chakwera omwe anali ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino a Joyce Banda pa tsiku lomwe anachititsa msonkhano wa atolankhani anapempha Amalawi kuti adekhe ndipo kuti pasadzakhale zipolowe chigamulocho chikaperekedwa.
A Billy Mayaya omwe ndi m’modzi mwa amkhalakale omenenyera anthu maufulu achibadwidwe komanso m’modzi wa akuluakulu a bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC, akuti Amalawi asaope kalikonse pa chigamulocho.
“Palibe chifukwa choopera ngati ndondomeko yofika pachigamulocho yalunjika pa chilungamo. Mantha angabwere pokhapo pamene pali mapulani ofuna kusokoneza chilungamo zomwe zingapangitse kuti ena asadzavomereze chigamulocho. Ngati izi zinachitike zingapangitsenso kuti anthu ena ayambitse zisokonezo zomwe Amalawi sakufuna,” anatero a Mayaya.
Iwo anati ndemanga zochuluka pa mulanduwu komanso chidwi chomwe anthu ali nacho pa mulanduwu zikutanthauza kuti Amalawi akufuna chilungamo “ndipo kutero sikukutanthauza kuti anthuwa akulakwitsa chifukwa akungofuna kuti chilungamo chioneke.”
Mkuluyu wati ngakhale kuti andale nawo pena amangolankhulapo pa nkhani zoterezi, ulendo uno andalewa akuyenera kuperekapo ndemanga zawo zomwe zikulimbikitsa kumanga osati kupasula.
“Mtendere ndiwofunika kwambiri ngati tikufuna kuti demokalase yathu izame komanso ipitirire kukomera Amalawi. Choncho andale ndi ena onse amene amalimbikitsa ulamuliro wabwino akuyenera kulimbikitsa mtendere,” anatero a Mayaya.
Ndipo a Ernest Thindwa, omwe ndi katswiri pa nkhani zandale ku sukulu yaukachenjede ya Chancellor, yomwe ndi nthambi ya Yunivesite ya Malawi, ati anthu akuyenera kusunga bata ndi mte-ndere kuyambira pano mpaka mtsogolo muno kaamba koti mtopola ndi nkhondo sidzimanga mudzi.
“Anthu akuyenera kusunga bata posatengera kuti chigamulo chikomera mbali yawo kapena ya enawo. Pa mlandu wina uliwonse pamayenera kupezeka owina ndi oluza. Chomwe chikufunika apa ndi kulemekeza chigamulo cha khoti posachita ziwawa kapena kulankhula mawu okhadzula omwe angabweretse chisokonezo. Tiyeni timange Malawi, tiyeni tilimbikitse umodzi,” anatero a Thindwa.
Mkuluyu wati nkofunika kuti aliyense adzavomereze chigamulo cha khoti ndipo kuti sikoyeneranso pa tsikulo kumadzachita zionetsero zotsutsana ndi chigamulochi kaamba koti uku kudzakhala ngati kunyozera malamulo a dziko lino.
A Thindwa anati anthu amapanga ziwonetsero ngati pali zifukwa zokwanira koma ngati palibe zifukwa palibe yemwe angakhale ndi mphamvu yochita ziwonetsero zotsutsana ndi chigamulo ngati chilungamo chayenda bwino.
Iwo apempha andale kuti pa nthawiyo adzadzichepetse ndi kulorerana kuti dziko lino lipite patsogolo pa ntchito zomwe zinasokonekera kaamba ka zionetsero ndi mlanduwu. A Thindwa anati atsogoleri andale adzachite zinthu zokonda dziko lawo ndipo izi zingatheke ngati pali mtendere.
“Njovu zikamamenyana umavutika ndi udzu. M’chimodzimodzi andale anthu akamakokana malaya ovutika ndi munthu wakumudzi yemwe akusowekera zinthu zofunika pa mowo wake monga mankhwala m’zipatala, madzi abwino ndi au-khondo ndi zina,” anatero a Thindwa.
A Eddy Kalonga omwe ndi m’modzi mwa aphunzitsi apa sukulu ya Malawi Institute of Management ndipo amatsata bwino m’mene ndale ndi zinthu zina zikuyendera muno mu Malawi komanso muno mu Africa, akuti palibe chifukwa chochitira ma-ntha nthawi imene khoti lipereke chigamulo pa mlandu wa chisankho chifukwa Amalawi ali m’dziko lawo.
“Chofunika ndi kusunga bata basi. Chodandaulitsa ndi choti anthu ena akuopseza amzawo pogwiritsa ntchito makina a Utatavu a mchezo monga Facebook ndi WhatsApp polenegeza za chigamulo cha bodza,” anatero a Kalonga.
Iwo adzudzulanso a ndale ena amene akulankhula mokhadzula pa nthawi imene akuyenera kulalika za mtendere. A Kalonga ati andale amene akulankhula mopasula ndi amene akuopseza mtendere umene wakhala pakati pa Amalawi zaka zonsezi.
“Malawi ndi wamkulu kuposa munthu wina aliyesense. Choncho tiyeni tipewe zipolowe ndi chisokonezo komanso kulankhula kosankhana mitundu,” a Kalonga atero.
Bungwe la HRDC lakhala likutsogolera zionetsero zofuna kuchotsa paudindo wapampando wa bungwe la MEC mayi Jane Ansah ati chifukwa sanayendetse bwino chisankho pa Meyi 21 chaka chatha.
Pa zionetserozi katundu wa ndalama zankhaninkhani wa boma, anthu wamba ndi mabungwe wakhala akuwonongeka. Anthu ena atayaponso miyoyo pa ziwawazi.
Anthu ali ndi chidwi kufuna kumva kuti mulanduwo ukomera ndani. Oweruza asanu aku khoti lalikulu (High Court ndi womwe akhala akumva nkhaniyi. Awa ndi a Healey Potani, Ivy Kamanga, Dingiswayo Madise, Redson Kapindu ndi Mike Tembo.