Chilema chodabwitsa… Zaka 20 akukulira pa mphasa
Wolemba: Precious Msosa
Pamakhala zinthu zina zoti zikakugwera pamoyo pena umatha kuyang’ana kumwamba nkudzifunsa kuti ‘Ambuye kodi muli kuti?’
Zimakhala zopweteka kwambiri akakhala kuti ndi matenda ndipo kupita kuchipatala palibe chomwe chimasintha. Umu ndi momwe banja lina m’boma la Blantyre likumvera.
Banja la a Nyson ndi Adola Nsomba am’mudzi wa Mphemvu Mfumu Yayikulu Kuntaja m’bomali liri ndi ana asanu ndi awiri (7) ndipo onse anabadwa bwinobwino kufikira pomwe awiri mwa anawa adakhala ndi chilema chodabwitsa.
Malingana ndi a Nsomba, Louis anabadwa walunga m’chaka cha 2000 kufikira m’chaka cha 2004 pomwe iye anadandaula za umodzi mwa miyendo yake. Iwo anati zitatero anamtengera ku bungwe lo-pereka chithandizo kwa ana la Cheshire Homes lomwe pano likutchedwa kuti Feed The Children.
A Nsomba anati atapita ku bungwelo, komwe anakhalako mwezi ndi theka, zinapezeka kuti mafupa ena a mwe-ndowo anali atasemphana kotero anatumizidwa kuchipatala cha mafupa cha Cure ku Blantyre komweko.
Kumeneko a Nyson anati madotolo anamuyika chikhakha koma sizinaphule kanthu mpaka Louis anayamba kuvutikiratu mayendedwe ake.
“Choncho anangotitulutsa ndipo kuyambira nthawi imeneyo (2005) mpaka pano, mavuto okhudza thupi lake akhala akukulirakulirabe mpaka kufika pokanikiratu kuyenda ndi kukhala,” anatero a Nsomba.
Iwo anapitiriza kufotokoza kuti asanayambe kukanikiratu kukhala, Louis anamuyambitsa sukulu pa pulaimale ya Nankuyu koma anangophunzira Sitandade 1 mpaka kalasi yachiwiri.
Apa a Nsomba anati iye sanakapitirize Sitandade 3 chifukwa samakhazikika bwino pa njinga yomwe bungwe la Cheshire Homes linamupatsa mchaka cha 2005 kaamba koti vutoli linali litayamba kukula.
“Kuyambira nthawi imeneyo, iye akumangokhalira chogona chifukwa akakhazikika msana umamupweteka,” anatero a Nsomba.
Koma iwo anati anafunitsitsa kuti Louis adziwe kulemba ndi kuwerenga choncho anawuza akulu ake azimuphunzitsa mpaka iye anadziwa kulemba ndi kuwerenga.
A Nsomba anati m’chaka cha 2009, Louis anapempha kuti amugulire foni ndipo atamugulira, foniyo inadzawonongeka koma chodabwitsa chake iye anakhonza yekha. Zitatero, anthu oyandikana nawo anayamba kubweretsanso mafoni kufikira panopa.
“Komabe pa nthawiyo ndinkamuletsa chifukwa ndimaopa kuti akawononga mafoniwo, zidzatsalira makolofe. Mwa chifundo cha Mulungu kunapezeka kuti akutha kukhonza komabe ali chigonere,” anatero a Nsomba.
Iwo anati akuthokhoza achifundo ena omwe amuthandiza ndi zipangizo zokhonzera mafoni mwezi watha.
Koma pamene anali kudandaula zavuto la Louis, banjali linabereka mwana womaliza Sella mu 2008, nayenso sipanapite nthawi pamene vuto lamayendedwe linamuonekera.
A Nsomba anati Sella anangodandaula za mwendo kupweteka ndipo atapita nayenso ku Cheshire Homes, vutoli silinatheke kulikhonza mpaka anafika polephereratu kuyenda.
Iwo anati kulekana ndi Louis, Sella akumatha kukhala yekha panjinga koma sukulu akumachita kumuphunzitsira panyumba abale ake chifukwa ku sukulu ya Nankuyu ndi kutali.
Iwo akuti sangathe kupeza mphu-nzitsi woti azimuphunzitsa chifukwa cha vuto la zachuma.
Atafunsidwa zomwe zinawaonekera anawa iwo anati, “ndikukhulupirira kuti ndi chipongwe cha anthu chifukwa kumbali ya kuchimuna kapena ya kuchikazi izi kulibe.
“Akuchipatala amaona ngati ndichoncho koma anali odabwanso titawauza kuti mbiri imeneyi tilibe.” “Chomwe tikufuna ndi thandizo kuti tikhale ndi bizinesi yodalirika kuti tiziwathandizira anawa. Ife ndi alimi ndipo ulimi siwodalirika zaka zino. Thandizo liri lonse tidzalandira,” iwo anatero.