Uncategorized

Dedza Dynamos ipilikitsa mphunzitsi

Timu ya Premier Bet Dedza Dynamos yalengeza kuti yachotsa ntchito mphunzitsi wawo Andrew Bunya kaamba ka kusachita bwino.

Woyendetsa ntchito za timuyi Guston Kamkosi Banda ndi amene walengeza izi lero mchikalata chomwe atulutsa timuyi itangogonja ndi Karonga United 4 kwa ndanda pa bwalo la Dedza.

Mwa masewero a mu Supa Ligi asanu ndi amodzi (6) omwe timuyi yasewera, iyo yapambanapo awiri ndi kugonja anayi ndipo ili pa nambala 10 ndi mapointi 6.