Isaac Liwotcha akufuulira thandizo
Wolemba: Watipaso CHIBWANA, Mtolankhani Wapadera
Mmodzi mwa oimba akale m’dziko muno, Isaac Liwotcha, akadape-mphabe chithandizo cha ndalama choti chimuthandizire kupita ku India kukalandira thandizo la matenda a fupa la ku msana, ‘spinal spondylosis’ pa Chingerezi.
Woimbayu yemwe anatchukapo kalero ndi chimbale chake cha Ambuye Mutimvere m’zaka zapakati pa 1995-1998 wakhala akulemba pa tsamba lake la mchezo la Facebook kuti akufuna kwabwino amuthandize koma izi sizikuphula kanthu.
Malingananso ndi uthenga wake watsopano wa pa tsamba lomweli la Facebook wa pa 14 December, 2025, Liwotcha wati unduna wa za umoyo umulipilira ndalama zakuchipatala koma apeze yekha mayendedwe okafikira ku dziko la ku India.

Liwotcha wasangalatsapo Amalawi ambiri ndi mayimbidwe ake (Chithunzi: Facebook)
Malingana ndi katswiriyu, pakufunika ndalama yokwana K16 miliyoni kuti apite ndi anthu awiri ku Chipatala chomwe si cha boma cha Yashoda m’dziko la India komwe akalandire thandizo lake.
Kusaonetsa chidwi chothandiza aluso athu makamaka oimba si nkhani yachilendo kaamba koti Amalawi ambiri amamukonda oimba akasamaya nkumadzanena zabwino zake pambuyo.
Izi zikutsatiranso zomwe a Paul Banda adutsamo kwa miyezi yapitayo pomwe akhala akudandaula za matenda awo kuti amasowekera thandizo la ndalama loti azigwiritsa ntchito popita ku chipatala cha Queens mu mzinda wa Blantyre koma zinangotengera Lawrence Khwisa (Lulu) kumema Amalawi kumuthandiza namandwayu.
Nawonso a Vita Chirwa womwe ndi mtsogoleri wa bungwe la oimba la Musicians Association of Malawi (MAM), anati khalidweli silabwino chifukwa litha kubwezeretsa mmbuyo aluso m’magawo osiyanasiyana.
A Chirwa anauza Mkwaso kuti oimba ndiamene amathandizira kukometsa dziko kaamba ka nyimbo zawo zomwenso zimasuntha anthu ambiri kotero kuti Amalawi azikhala ndi danga lokuta aluso awo pa mavuto ndi pa mtendere pomwe.
Mu nyimbo ya ‘Ambuye Mutimvere’, Liwotcha amapempha Mulungu kuti amve madandaulo ndinso mavuto omwe anthu akukumana nawo m’miyoyo yawo ya tsiku ndi tsiku.
Ofuna kulumikizana ndi woimbayu atha kumupeza pa nambala iyi: 0999 449 502.
