Nkhani Zina

Khonsolo ya Balaka ivomereza pulojekiti yothandiza kuchepetsa njala

Komiti yayikulu ya boma la Balaka lachisanu inavomereza pulojekiti yothandizira kuchepetsa njala komanso kunyentchera yomwe bungwe la Save the Children ikufuna kukhazizitsa m’bomali.

Malingana ndi a Steve Kamtimaleka, womwe ndi mkulu woona zothandiza anthu komanso kagwiridwe ka ntchito ka m’madera ku bungweli, pulojekitiyi yomwe mchingerezi ikutchedwa “Malawi Drought Response,” ili pansi pa mgwirizano wa mabungwe angapo kuphatikizapo la Save the Children omwe ukutsogozedwa ndi bungwe la CARE ndi thandizo la ndalama lochokera ku bungwe la European Union.

 Iwo ati pulojekitiyi idzipereka thandizo la ndalama kwa anthu okhudzidwa ndi njala komanso uphungu wa kadyedwe koyenera ndipo mabanja 2,560 ndi omwe akuyembekezeka kufikiridwa ku Balaka.

 “Pulojekitiyi kwambiri ithandizira kuchepetsa njala komanso kunyentchera, monga mukudziwa chaka chatha chonsechi dziko la Malawi linakhudzidwa ndi ng’amba ya El Nino.

“Tigwira ntchito ndi amnzathu a chipatala owona za madyedwe abwino kuti anthu aonetsetse kuti akuphika chakudya chamagulu asanu ndi limodzi (6),” anatero a Kamtimaleka.

M’mawu awo , mkulu woona za Ulimi komanso chilengedwe mu khonsolo ya Balaka, a David Alli, anati pulojekitiyi ayilandira chifukwa choti njala m’bomali ndiyambiri.

 “Kubwera kwa pulojekitiyi kutithandizira kuti mabanja okhudzidwa ndi njala akhale ndi mwayi wolandira chakudya, komanso akhale ndi madyedwe abwino omwe athandizire kuchepetsa kunyentchera,” anatero a Alli.

Pulojekitiyi ikuyembekezeka kupindulira anthu a m’madera omwe ali pansi pa mfumu yayikulu Nkaya, Chamthunya, komanso Phimbi ndipo igwiritsa ntchito ndalama zokwana K861, 434,344. Ena mwa maboma omwe apindule ndi pulojekitiyi ndi monga Zomba, Nsanje komanso Mangochi.

Wolemba: Cytress Kaunda