Ma Queens aphwanyitsa mutu
Wolemba: Precious MSOSA
Mpikisano wa mpira wa manja, wa Africa Netball Cup, unafika pa kamuthemuthe pa 14 Disembala, 2025 pa bwalo la Griffin Saenda Sports Complex, mu mzinda wa Lilongwe ndi timu ya South Africa kukhala akatswiri m’magawo onse a mpira wa manja wa atsikana, komanso wa anyamata.
Timu ya Uganda nayonso inateteza malo ake, pomwe inathera pa nambala yachiwiri kutsatira kugonja ku timu ya South Africa, mu ndime yomaliza ya mpikisanowu, womwe unayamba pa 8 Disembala.
Atsikana a timu ya Zimbabwe anathambitsa Malawi ndi zigoli 48-44 kuti athere pa nambala yachitatu. Zotsatira za masewerowa zinadabwitsa anthu ambiri otsatira masewero a mpira wa manja, pokhala kuti Zimbabwe ilibe mbiri yoopsa kumbali ya masewerowa.
Koma malingana ndi anthu okonda mase-werowa, kugonja kwa timuyi kwa Zimbabwe kukuyenera kupereka uthenga kuti zinthu sizili bwino ku mbali ya ma Queens.

Ena mwa osewera a timu ya Malawi (Photo Credit: NAM)
Malingana ndi ena mwa anthuwa, omwe amapereka maganizo awo pa tsamba la mchezo la Facebook la Malawi Netball, tsopano nthawi yakwana yoti timuyi iyesere mphunzitsi wa ku maiko odziwika bwino pa masewerowa, monga Australia ndi England, mwa ena.
Koma Waile Juma, m’modzi mwa anthu omwe analemba pa tsamba la Facebook la Malawi Netball, anati ganizo lopeza mphunzitsi wa kunja silabwino kwenikweni, kaamba koti pazidzakhala kuvutika kumbali yolumikizana bwino ndi osewera kumbali ya chiyankhulo. Iye anati kulibwino kusiya momwe zililimu chifukwa tsogolo likuwoneka.
“Mukamaganiza za mphunzitsi wa kunjazo tidzapezeka nazo pa nambala 8, tiyeni tivomereze kuti tathera pa nambala yachinayi. Ndizotheka kudzathera pa nambala yachiwiri kutsogoloku,” anatero Juma.
Naye Lilly Soko anati akukhulupirira kuti timuyi ilibwino koma pakufunikira kukonza ndi malo ochepa monga kumbuyo. Maganizo a Lilly ndiwomwe anthu ena akugwirizana nawo ponena kuti timuyi ikufunikira otchinga kumbuyo olimba mtima ngati Caroline Mtukule Ngwira komanso Towera Vinkhumbo Nyirenda.
“Ndikuwona ngati tikufunikiranso kwambiri otchinga kumbuyo a mphamvu, komanso oti adzitha kudula mipira pomwe pakufunika kukokera; Towera ndi Carol izi kunali kudya kwawo. Komanso mdani wako nthawi zina amazafunika ka nyumwisa pang’ono, zomwenso awiriwa amadzitha kwambiri,” anatero Chisomo Ngulube, yemwe ndi mtolankhani wotsatira bwino za masewero.
Malingana ndi mphunzitsi wa timuyi, Peace Chawinga Kalua, ena mwa osewera atsopano alibwino ndipo ali ndi tsogolo labwino, zomwe zikupereka chiyembekezo ku timuyi.

Chawinga-Kalua: Ena mwa osewera atsopano alibwino ndipo akupereka chiyembekezo (Photo Credit: NAM)
Koma iye anati osewerawa akungoyenera kuphunzira kudekha masewero akafika potentha chifukwa izi ndizomwe zinachititsa kuti timuyi igonje kwa Zimbabwe.
Mwa masewero anayi, timu ya Queens ina-kwanitsa kupambana masewero awiri, a Botswana 46-42 komanso Tanzania 55-34. Iyo inagonja kwa South Africa 38-58 ndinso kwa Zimbabwe 44-48.
Poyankhulapo pa za mpikisanowo womwe unabweretsa pamodzi maiko asanu ndi atatu (8), wapampando wa komiti yomwe imakonza mpikisanowu mdziko muno, a Limbani Matola anathokoza onse omwe anabwera kudzaonera masewerowa.
Iwo anathokozanso makampani onse omwe anathandizira kuti mpikisanowu uyende mwa dongosolo.
