Mkangano wovala hijabu ufika pa mapeto
Wolemba : Precious Msosa
Kwa nthawi yayitali nkhani ya chovala cha hijabu yakhala ikubweretsa mikangano makamaka mu sukulu zachikhristu, koma pano zonsezi ndi mbiri yakale kutsatira pangano lomwe akuluakulu a mabungwe a Chikhristu ndi Chisilamu asayinirana pa nkhani ya chovalachi. Mgwirizanowu wabwera boma litapempha bungwe la zipembedzo zosiyanasiyana la Public Affairs Committee (PAC) kuti lithandizire kulunzanitsa akhristu ndi asilamu m’boma la Machinga omwe anali pa nkhondo kaamba koti eni sukulu ya pulaimale ya Mpiri samaloleza
ophunzira achitsikana kumavala hijabu ku sukulu. Mkanganowu unafika poyipa kwambiri mpaka asilamu anawononga
katundu wina pa sukulupo komanso anawopseza kuthamangitsa ndi kutseka parishi ya Katolika ku Mpiri. Sukuluyo eni ake ndi a Mpingo
wa Katolika. Koma malingana ndi panganoli, atsikana tsopano ndiololedwa kumavala hijab m’sukulu za Chikhristu koma chovalachi chidzifanana ndi yunifolomu. Mu panganoli, atsikana omwe akuphunzira m’sukulu za chisilamu siwololedwa kukakamizidwa
kuvala hijabu. Poyankhula pa mwambo wosayinira panganoli ku Blantyre posachedwapa, wachiwiri kwa wapampando wa PAC a Osman
Karim anati sichinali chophweka kufika pamenepa. Iwo anati nthawi zina zokambiranazi zinatsala pang’ono kulephereka chifukwa
cha kusakhulupirirana. “Panganoli palokha silingathetse mikangano koma mitima ndi maganizo athu akhale olunjika ku mtendere ndi umodzi. Ngati ziwawa zilizonse zingabwere mokhudzana ndi nkhaniyi (hijabu), apolisi akuyenera kuchitapo kanthu,” anatero a Karim.
Mmodzi mwa akuluakulu ku bungwe la Muslim Association of Malawi (MAM) a Sheikh Ali Kennedy anati mkangano uliwonse wokhudzana ndi kusiyana kwa zipembedzo kapena kochokera umakhala ndi zotsatira zowononga kwambiri. “Ndine wosangalala kwambiri
kuti tsopano nkhaniyi yatha. Ndiyamikirenso mtsogoleri wa dziko lino powonetsa chidwi kuti nkhaniyi ithe mwa mtendere.” Wapampando wa bungwe la maepiskopi la Episcopal Conference of Malawi (ECM) Ambuye Thomas Msusa, omwenso anayimirira bungwe la Association of Christian Educators in Malawi (ACEM), anati ndizosangalatsa kuti tsopano pali pangano lokha-zikika pankhani ya
hijabu m’sukulu. “Tikuyenera kumakumbukira kuti pa mkangano uliwonse pamakhala okhudzidwa ndipo pa mkanganowu omwe anapwetekedwa ndi ophunzira pa sukulu ya Mpiri omwe akhala pafupifupi chaka asakuphunzira zomwe si chinthu chabwino,” anatero Ambuye Msusa. Nduna yophunzitsa anthu ntchito zosiyanasiyana ndi kulimbikitsa umodzi a Timothy Mtambo anati ndikofunika kutengera panganoli kwa anthu kumadera kuti nawonso amvetsetse ndi kutsatira zomwe magawo awiriwa agwirizana.