Uncategorized

Ngumuya wadzambatuka ndi “Adzakhala Adzakhala”

Wolemba: Victor SINGANO Junior, Mtolankhani Wapadera

Atatulutsa chimbale mchaka cha 2014 chambakale pamaimbidwe a nyimbo zauzimu Allan Ngumuya wavumbulukanso ndi chimbale chatsopano chotchedwa ‘Adzakhala Adzakhala’ chomwe chili ndi nyimbo khumi.

Ngumuya yemwenso anakhalapo phungu waku Nyumba yaMalamulo kudera la kum’mwera kwa tauni ya boma la Blantyre tsopano wakwanitsa chimbale cha khumi ndi mphambu zisanu (15) ndipo wakhala zaka 35 akugwira ntchito yoimba.

Muchimbale chatsopanochi mulinso nyimbo zina zomwe zongoonjezera zokwana khumi zomwe zachokera mu zimbale zakale.

Ngumuya: Anthu ayembekezere kuyamba kugula chimbale tsiku lirilonse

Ngumuya wauza Mkwaso kuti zina mwa nyimbo zomwe zili mchimbalechi chomwe chifike pamsika mwezi uno wa Janyuwale wayimba motha-ndizananso ndi oimba ena monga Lucius Banda, Wycliffe Chimwendo, Chifundo Chiwaya, Carlo Dzuwa komanso  gulu la Mixed Voices la mpingo wa Saventh Day.

“Anthu ayembekezere kuyamba kugula chimbale tsiku lirilonse kuyambira mwezi uno wa Janyuwale ndipo chizipezeka mu mashopu a malo omwetsera mafuta, ma Bookshop komanso pa makina a intaneti. Posachedwapa ndikhala ndikujambula nyimbo zowerengeka zowonera,”anatero Ngumuya.

Chimbalechi chili ndi nyimbo ngati Nkhosa, Galilea, Pali Bwenzi mongotchulapo zochepa.

Ngumuya anatulutsa chimbale chake choyamba mchaka cha 1985 chotchedwa ‘Mtanda’.