Nyanga ya Kudu ya K7 miliyoni ipititsa abambo awiri ku ndende
Bwalo la milandu m’boma la Balaka lalamula anthu awiri kupita ku ndende pa mlandu wopezeka ndi nyanga iwiri ya nyama ya Kudu ya ndalama zokwana K7 miliyoni popanda chilolezo.
Abambo awiriwa ndi a Bright Chiwaya a zaka 39 womwe woweruza mlanduwo a Joshua Nkhono awalamula kuti akagwire ukaidi wa miyezi 60 komanso a Ishmael Benard a zaka 24 womwe awalamula kuti akakhale ku ndende kwa miyezi 48.
Malingana ndi wofalitsa nkhani za apolisi m’boma la Balaka a Gladson M’bumpha, bwaloli linamva kuchokera kwa woyimira boma pa mlanduwo a Bodwin Msukwa kuti pa 16 Febuluwale chaka chino abambo awiriwa anapezeka ali ndi katunduyu m’mudzi wa Kapile popanda zikalata zowaloleza kutero.
A M’bumpha anati mlanduwu utalowa mu khoti, awiriwa anawuvomera zomwe zinapangitsa kuti iwo apatsidwe chilangocho. Koma mneneri wa apolisiyu anati a Benard apatsidwa chilango chochepa chifukwa ndiamene anali ngati mkhalapakati (agent) wogulitsa minyangayo.
A Chiwaya amachokera m’mudzi wa Manjawira mfumuyayikulu Tsikulamowa m’boma la Ntcheu pomwe a Benard amachokera m’mudzi wa Kamvalutope mfumu yayikulu Matola in Balaka.