Polisi ya Lilongwe yamanga anthu 11
Polisi ya Lilongwe yamanga anthu khumi ndi m’modzi powaganizira kuti anaba zinthu kwa mnyamata wina wa zaka 17 wa ku China.
Malinga ndi ofalitsa nkhani za apolisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu, omangidwawa ndi a Daniel Kudzala a zaka 33, a Reuben Kankhuni a zaka 32, a Ranken Msakambewa a zaka 38, a Steven Mpakati a zaka 57, a Emmanuel Smart a zaka 37, a James Amadu a zaka 38, a Robert Kaiwalika a zaka 32, a Davie Kalipinde a zaka 40, a Emmanuel Phiri a zaka 32, a Esau Phiri a zaka 48, ndi a William Lodistala a zaka 32.
Iwo ati pa tsikulo, nthawi ya 6 koloko madzulo, zigawenga 16 zomwe zinali ndi zikwanje zinafika pa kampani ina komwe anamenya ndi kumangirira mwana wa eni kampaniyo ndipo kenaka anamubera lamya ndi ndalama zomwe zinali mu ofesi ya wolandira ndalama.
A Chigalu ati zigawengazo zinkagwiritsa ntchito minibus yomwe nambala yake ndi LA 7229 yomwe ndi ya a Daniel Kudzala omwe ndi woganizilidwa woyamba – ndipo cholinga chawo chinali kuba sefa yomwe amakhulupirira kuti munali ndalama zambiri atatsinidwa khutu ndi a Reuben Kankhuni, yemwe ndi mekaniki wa kampaniyo.
Koma anthuwa anakanika kuba kaamba koti amayi a mwanayo, omwe anali malo obisika, anawomba mfuti zomwe zinawachititsa mantha ndipo anathawa.
Atafunsidwa anthuwa avomereza kuti Kankhuni ndi amene anayamba kufalitsa uthenga woti kampaniyo inali ndi ndalama zambiri mu sefa, chifukwa amakhala nthawi yaitali osapititsa ndalama kubanki ngakhale amalandira ndalama zambiri kuchokera ku malonda a miyala.
Malingana ndi a Chigalu, a Daniel Kudzala anayambitsa magulu atatu a zigawenga ochokera ku madera a Area 23, Mgona ndi tawuni ya Lilongwe, ndipo ndi amene anakonza zokabera kampaniyo.
Zinadziwikanso kuti zigawengazi zinachita misonkhano iwiri yokonzekera ku bwalo la zamasewero la Lilongwe Teachers College komanso ina ku Naele.
Wina mwa katundu yemwe anabedwa ndi foni ya iPhone yamtengo wa K3.5 miliyoni ndi ndalama zokwana K250,000 ku kampani ya ZZTH Wealth ku Nathenje pa 25 Epulo chaka chino, akubawa atakanika kuthyola sefa yosungira ndalama.
Pakadali pano, apolisi akusakasaka anthu ena omwe anathawa kuti chiwerengero cha zigawenga chifike pa 16.