MkwasoNkhani Zina

SEED idandaula ndi kuchepa kwa ndalama

Wolemba: Precious MSOSA

Nthambi ya maphunziro ku chigawo chakumwera kummawa (South East Education Division (SEED) yadandaula ndikuchepa kwa gawo la ndalama lomwe imapatsidwa zomwe zikudzetsa mavuto ku mbali yokonzanso sukulu m’chigawochi.

Poyankhula pomwe komiti ya ku Nyumba ya Malamulo yoona za maphunziro inayendera sukulu ya sekondale ya Balaka, wamkulu woyang’anira nthambi ya SEED a Edna Manyungwa anati ndalama zokwana K100 miliyoni zomwe amapatsidwa sizokwanira kuti nthambiyi ikwanitse kukonza sukulu zonse zomwe zinawonongeka m’chigawochi.

Iwo anati pa sukulu 154 zomwe zili m’chigawochi, ndalamayi ndiyochepa kwambiri potengera zosowekera zomwe zimakhalapo m’sukulu zosiyanasiyana.

A Manyungwa amayankhapo pa zomwe wophunzira wina pa seko-ndale ya Balaka anauza komitiyi kuti limodzi mwa mavuto aakulu pa sukuluyi ndi kuonongeka kwa malo ogona (hostel) komanso mabedi ndi matiresi ogonera.

Manyungwa: Atiganizire (Chithunzi: Precious Msosa)

“Mavuto ngati awa akumabwera kaamba koti ndalama zomwe timapatsidwa pa chaka sizikumakhala zokwanira. Sizikumatheka kuti pa ndalama yokwana K100 miliyoni yomwe timapatsidwa kuti tiyendetsere maphunziro m’chigawochi, pomweponso tikuyenera kuchotsaponso gawo lina lokonzetsera sukulu zomwe zaonongeka,” anatero a Manyungwa.

Choncho iwo anati ndikofunikira kuti boma makamaka, Unduna wa Maphunziro uganizire zomapereka ndalama zapadera za thumba lokonzetsera sukulu zomwe zaonongeka (maintenance fund) kapena kungokweza thumba la ndalama zomwe amapereka.

Iwo anati ngati sichoncho, ndibwino kuti ntchito yokonza zinthu zikulu zikulu zomwe zaonongedwa pa sukulu izigwiridwa ndi a ku unduna kuti iwo adzingokonza zinthu zing’onozing’ono.

Poyankhapo pa ma dandauloli, wapampando wa komiti yoona za maphunziro ku Nyumba ya Malamulo a Mutani Tambala anagwirizana ndi ganizo loti ntchito zikulu zikulu zokonza sukulu zomwe zaonongedwa zizi-gwiridwa ndi a ku unduna.

A Tambala anati zomwe yapeza komitiyi pa ulendo wawo wa ku Balaka komwenso inakayendera sukulu ya sekondale yoyendera ya St Louis komanso m’boma la Salima akaziyika mu lipoti ndicholinga kuti adindo ena akazilingalire.

Mgwirizano wa mabungwe woona za ufulu wa ana wa Non-Governmental Organization (NGO) Coalition on Child Rights ndiwomwe unakonza maulendowa mogwirizana ndi bungwe la Unicef.