Sitikubwerera m’mbuyo pa chitukuko – Khonsolo ya Balaka
Wolemba: Joseph KAYIRA
Boma la Balaka lakhala likuchita bwino pa chitukuko ndipo ulendo wina linasankhidwa kukhala akatswiri odziwa kulondoloza bwino zitukuko za thunga la Governance to Enable Service Delivery (GESD). Chaka china linadzakhala lachiwiri poyendetsa bwino ndalama za thumbali. Koma zinthu zinazasintha pomwe bomali linapezeka kuti linatenga ndalama za ku thumbali nkukathandizira ku chipatala chachikulu chomwe chinakumana ndi ngozi ya moto.

Nawata kupereka lipoti la zitukuko zomwe zachitika m’boma la Balaka (Chithunzi: Joseph Kayira)
Moto utatentha mbali ina ya chipatala cha Balaka — maka kumbali yokonza zakudya — ku khitchini — khonsolo inaganiza zotengako ndalama zina za GESD kukathandizira kugula miphika yaku chipatala yomwe inali itawonongeka ndi moto.
Nkhaniyi siinakondweretse omwe amayang’anira thumba la chitukukoli. Izi zinachititsa kuti boma la Balaka lisemphane ndi ndalama pafupifupi K600 miliyoni za chitukuko. Malingana ndi malamulo oyendetsera thumbali khonsolo ya boma la Balaka siimayenera kutapa ndalama za mthumbali nkukathandizira ku chipatala mwa ilo lokha — ngakhale kuti kuthandizako sikunali kolakwika.
Khonsoloyi itaphunzirapo pa kulakwa kwake tsopano yakangalika kuyala zitukuko ndipo siikubwerera m’mbuyo. Mwa zina, khonsoloyi ikumanga masukulu, misika, zipinda zochirira amayi pa zipatala zina, komanso kumanga maofesi abwino — mongotchulapo zochepa.

Chitsulo: Boma la Balaka likuchita bwino pa chitukuko (Chithunzi: Joseph Kayira)
Izi zaululika pomwe wachiwiri kwa nduna yoona za maboma aang’ono, umodzi ndi chikhalidwe, a Joyce Chitsulo anayendera zina mwa zitukuko za m’khonsoloyi Lachinayi, pa 13 Febuluwale 2025. Ndunayi inati zomwe zinachitika pomwe khonsoloyi inalephera kulandira ndalama za chitukuko za GESD kunachititsa kuti liphonyane ndi chitukuko cha nkhaninkhani.
“Chifukwa cha zimene zinachitikazo, khonsolo ya Balaka inasemphana ndi ndalama zokwana K600 miliyoni za chitukuko. Ndikofunika kutsatira ndondomeko za chitukuko monga m’mene zinakhazikitsidwira. Izi zimathandiza kuti chitukuko chiziyenda mwa dongosolo komanso mogwirizana ndi malamulo.
“Koma ndine wokondwa tsopano kuona m’mene boma la Balaka lasinthira. Khonsolo ikuyesetsa kukhazikitsa zitukuko zochititsa chidwi, pena nkumati; ndi ku Balaka konkuno? Ndayendera zipinda zochiriramo amayi pa chipatala cha Kwitanda komanso pa chipatala cha Chiendausiku. Ndi zipinda zapamwamba kwambiri ndipo ndikuyamikira khonsolo chifukwa chozipereka motere,” anatero a Chitsulo.

Harawa: Zonse zikuyenda bwino tsopano (Chithunzi: Joseph Kayira)
Ndunayi yapemphanso kuti anthu aku Balaka ayambe kulondoloza zitukuko zawo ndipo akawona kuti zinthu siziyenda monga m’mene anauzidwira, iwo ali ndi ufulu wofunsa adindo chomwe chikuchedwetsa zitukukozo.
“Mafumu athu mulinso ndi ntchito yofunsa pomwe zinthu zikulakwika. Makhansala ndi Aphungu a Nyumba ya Malamulo muyeneranso kugwirana manja kuti zinthu ziyende monga m’mene anthu akuyembekezera. Nonse mukufuna chitukuko ndipo pasakhale mikangano.
“Nthawi zina kontirakita amachedwetsa ntchito ndipo anthu amangoyan’gana mpaka zinthu kuonongeka. Kontirakita ngati akuchedwetsa ntchito, muchotseni, lembani wina. Osalekerera mpaka zinthu zionongeke. Akachedwetsa zinthu ndi aja amadzabweranso kuti simenti yakwera ndiye akufuna ndalama yapamwamba. Ndalama yapamwambayo apereke ndani?” anatero a Chitsulo.
Tayamba mwatsopano
Khonsolo ya boma la Balaka yatsimikiza kuti tsopano yakangalika kusintha zinthu kuti isaphonyanenso ndi ndalama za chitukuko monga m’mene zinachitikira m’mbuyomo. Iyo yati ikuyesetsa kuti matumba onse amene kumachokera ndalama za chitukuko aziyenda mwadongosolo. Mwa ena, bomali limalandira ndalama kuchokera ku GESD, District Development Fund (DDF), Hospital Rehabilitation Fund, Constituency Development Fund (CDF) ndi ena.
Bwanamkubwa wa boma la Balaka, a Tamanya Harawa anati iwo sakuonanso za m’mbuyo koma kupita chitsogolo ndipo ntchito za chitukuko zimene anaziyala mzaka zinayi zapitazo zatha mwadongosolo.

Ndebele m’chipinda chochirira amayi pa chipatala cha Kwitanda (Chithunzi: Joseph Kayira)
“Pa kulephera kopeza ndalama za GESD m’mbuyomo, omwe analakwitsawo sikuti anachita mwadala ayi. Inali ngozi kaamba koti ndalamayo inakagwira ntchito inanso yofunika ku boma konko. Koma kupita chitsogolo ndinganene mosaopa kuti zonse zikuyenda bwino,” iwo anatero.
Iwo ati pakali pano khonsolo ya Balaka ikutsatira bwino ndondomeko zonse zachitukuko ndipo pali chiyembekezo choti zitukuko zosiyanasiyana zikhala zikufikira anthu a m’madera osiyanasiyana m’bomalo.
Mkulu woona ntchito za chitukuko mu khonsolo ya Balaka, a Chris Nawata agwirizana andi a Harawa ponena kuti boma la Balaka tsopano likuchita bwino pa chitukuko. Popereka lipoti la zaka zinayi la khonsolo ya Balaka, a Nawata anati khonsoloyi yaphunzira zambiri ndipo tsopano yalunjika powonetsetsa kuti zitukuko zomwe zaikidwa zizitha mu nthawi yake.
Iwo anati khonsoloyo ili paubale wabwino ndi mabungwe osiyanasiyana ndipo izi zikuthandizanso kuti zitukuko ziziyenda mwadongosolo m’bomalo.
“Pano tikhala tikupindulanso kudzera mmatumba osiyanasiyana a chitukuko. Tikufuna kuti m’tsogolomo anthu azizanena kuti anthu awa anagwira ntchito yotamandika mu nthawi yawo. Tikukamba za zitukuko zosiyanasiyana zomwe zikamabwera cholinga chake chimakhala choti anthu a m’bomali apindule nazo,” anatero a Nawata.
Phungu wa Nyumba ya Malamulo wa Dera la ku Zambwe kwa Balaka, a Bertha Ndebele anati ndi zosangalatsa kuti chitukuko chayamba kuyenda bwino m’bomali. Iwo afotokoza kuti maboma a m’mbuyomu amanyalanyaza kubweretsa zitukuko koma pano zinthu zinasintha.

Chipinda chamakono pa chipatala cha Chiyendausiku (Chithunzi: Joseph Kayira)
“Pano zipatala zamangidwa ndipo zasintha miyoyo ya amayi. Kale anthu amatha kukakhala ku chipatala chachikulu kwa miyezi akudikirira kuti munthu achire. Pano zipatala zamangidwa kumudzi komweko monga m’mene zilili kwa Chiyendausiku ndi kwa Kwitanda. Izitu ndi zina mwa zitukuko zomwe anthu akufuna,” anatero a Ndebele.
Phunguyu wati ndalama za GESD zathandiza kwambiri pa chitukuko m’bomalo ndipo ali ndi chikhulupiriro kuti izi zipitirira mokomera anthu.