Zaka 100 za chisoni ndi chimwemwe pa sukulu ya Bazale

Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA

Aphunzitsi ndi ana akusimba lokoma pa sukulu ya pulaimale ya Bazale yomwe ili mdera la mfumu yaikulu Msamala m’boma la Balaka. Kwa zaka za-mbiri sukuluyi yakhala ili yoiwalidwa, yopanda makalasi abwino ndipo ana amasiyila sukulu pa njira. Koma lero zonsezo ndi mbiri yakale a Montfort Projects mothandizana ndi abwenzi aku Ulaya atamanganso ndi kukonza zomwe zinaonongeka pa sukuluyi. Sukuluyi inatsegulilidwa mchaka cha 1920 ndi mpingo wa Zambezi Evangelical.

Nthawi imene mpingowu unkayendetsa sukuluyi ati zonse zinali bwino opanda vuto lina liri lonse monga kusowa kwa makalasi, aphunzitsi ndi zina. M’chaka cha 1973 sukuluyi inaperekedwa m’manja mwa boma kuti lidziyisamalira. Zinthu zinali kuyenda bwino mpaka nthawi yomwe sukuluyi inatsala ndi mdadada umodzi omwe amagwiritsa ntchito kwa zaka zambiri.

Makolo ozungulira sukuluyi anaganiza zomanga mdadada wina powumba okha njerwa komanso mothandizidwa ndi mkulu wina ochita bizinesi m’bomali, a Patrick Simon ndi banja lawo, ngati njira imodzi yochepetsera vuto la makalasi. Ngakhale izi zinali chonchi sizinaphule kanthu pa sukuluyi chifukwa maphunziro amasokoneke-rabe, zomwe zimachititsa ana kusachita bwino mkalasi komanso kuweluka msanga.

Mdadada watsopano pa sukulu ya Bazale

Malingana ndi phunzitsi wamkulu pa sukuluyi, a Hussein Nkhata, zaka 100 za sukuluyi ndi zachisoni komanso chimwemwe poti sukuluyi pano yavala nkhope yokongola zomwe akhala akuzisowa kwa zaka zambiri.

“Mwana kuti aphunzire komanso achite bwino, sukulu imafunika izikhala ndi zipangizo zokwanira osati m’mene inaliri sukuluyi. Ophunzira samakhala ndi chidwi chifukwa cha amaonekedwe ake,” anatero a Nkhata.

A Nkhata anati ngakhale sukuluyi inali ndi mavuto adzaoneni aphunzitsi amagwirabe ntchito yosula ana kuti azakhale nzika zodalilika posatengera mavuto omwe akukumana nawo.

“Pano pali nyumba za aphunzitsi ziwiri zokha. Aphunzitsi ambiri amachokera kutali zomwe zimachititsanso maphunziro kusayenda bwino chifukwa amakhala atatopa ndiye samaphunzitsa mokwanira,” anatero a Nkhata.

Mbiri ya sukuluyi inapita patali chifukwa inalibe makalasi abwino ndipo ophunzira ambiri amachita manyazi kutchula ku sukulu komwe akuphunzira kuwopa kusekedwa ndi anzawo omwe akuphunzira sukulu zowoneka bwino komanso zomwe zili ndi zipangizo zowoneka bwino.

“Mukamadutsa pano zoti panali sukulu sizimaoneka zomwe zimachititsa ophunzira kuthawa mkalasi kupita kumakaonera kanema. Ena kumakavina m’midzi nthawi ya chinamwali akamva kuyimba ng’oma mmalo mophunzira,” anatero a Nkhata.

M’modzi mwa ophunzira, Chimwemwe Batumeyo, anati moyo pa sukuluyi unali owawa chifukwa chophunzira pa mtengo nthawi ya dzinja ndi chilimwe.

“Zovala zathu zimada komanso sitimakhala ndi chidwi chomvetsera tikamaphunzira pa mtengo. Timakhala tikuwona zochitika ku msewu ndi zina,” anatero Batumeyo.

Batumeyo anati pano ndi wosangalala chifukwa sukuluyi yalandira mdadada wa makalasi asanu ndi atatu apamwamba zomwe zithandize ophunzira kumakhala malo abwino ophunzirira kulekana ndi m’mene amaphunzirira pa mtengo zomwe zimasokoneza maphunziro.

“Pano kulibe kuweluka msanga chifukwa cha dzuwa ndi mvula chifukwa makalasi omwe atimangira ndi apamwamba ndipo unifolomu sizida ngati kale,” anabwekera Batumeyo.

Mkulu woona ntchito za maphunziro m’boma la Balaka, a Ignitious Kameni, ati ndi wokondwa ndi mphatso ya mdadada wa tsopano womwe alandira zomwe zithandize kuchepetsa mavuto amakalasi.

“Mdadada womwe talandira ndi sukulu kale payokha chifukwa ndi wamakono komanso atipatsa zonse zoyenereza kukhala mkalasi. Izi zithandizanso kuchepetsanso kufala kwa matenda monga a Covid-19 chifukwa ophunzira azikhala motalikirana kusiyana ndi kale pomwe ana amakhala mothithikana chifukwa chosowa makalasi,” anatero a Kameni.

A Kameni anapempha makolo ndi ena kuti asamalire sukuluyi osati kuba zipangizo mkumakagulitsa.

“Makolo tumizani ana ku sukulu osati azingokhala m’makomo. Pano kulibe chonamizira kuti ana akujomba chifukwa chosowa makalasi abwino. Komanso anawa asamangokhala pakhomo kuchita makhalidwe osayenera m’malo mobwera kudzaphunzira kuno,” anatero a Kameni.

Iwo anati, kwa omwe anasiya sukulu, nthawi yakwana yoti abwe-rere ku sukulu chifukwa sukuluyi pano ili ndi makalasi ambiri kuposa kale. Ophunzira ambiri pa sukuluyi anasiya kupita ku sukulu chifuwa cha vuto la makalasi maka atsikana omwe amachita manyazi kukhala pansi komanso nyengo zawo zikakhala sizili bwino samabwera chifukwa panalibe mabafa oti azidzisamalira.

A Kameni anathokoza ntchito yomwe Montfort Projects ikugwira yotukula maphunziro m’bomali zomwe boma palokha silingakwanitse koma zikutheka chifukwa cha anthu ena omwe akutenga nawo mbali yolimbikitsa maphunziro.

Chitukuko chikamabwera pamalo anthu amakhala ndi zikhulupiliro zosiyanasiyana. Ena amaganiza kuti ngati akubweretsa chitukuko ndi ampingo  ndiye kuti akufuna kuwakopa kuti alowe chipembedzo chawo kuyiwala kuti akuthandiza posatengera chipembedzo chawo. Izi ndi zomwe Montfort Projects, yomwe imakonza sukuluyi inakumana nazo chifukwa anthu ozungulira sukuluyi anali ndi maganizo awo.

Kameni: Mdadada watsopano wathetsa umphawi wamakalasi

Ngakhale izi zinali chomwechi mkulu oyang’anira Montfort Projects, Bambo Piergiorgio Gamba sana-bwerere m’mbuyo koma kuwawuza anthuwa kuti amvetsetse cholinga chomwe akukonzera sukulu chomwe kunali kufuna kuti ana ayambe kuphunzirira pamalo abwino komanso opereka chikoka osati kuwakokera ku chipembedzo chawo.

Pano ndi chimwemwe chokhachokha kuti umphawi wa makalasi watha kudzera kwa abwenzi amayiko a Italy ndi Spain, a San Marino, Caritas Antoniana ndi Manus Unidas omwe anathandiza kukonza sukuluyi kudzera ku Montfort Projects.

Abwenziwa anakonzanso ofesi ya mphunzitsi wa mkulu, mjigo, nyumba yowerengeramo, mpanda komanso ayika magetsi pa sukuluyi kuti aziwunikira. 

M’bomali muli sukulu za pulayimale zoposa 200 ndipo zambiri muli mavuto adzaoneni.

Ndi sukulu zochepa zokha zomwe zili ndi zipangizo monga makalasi abwino ndi zina. Mwa ophunzira  m’sukulu za pulayimale m’bomali,  atsikana  alipo ochuluka kuposa anyamata. Sukulu ya Bazale ili ndi aphunzitsi makumi asanu ndipo ambiri ndi azimayi.