Zaka 58 za ufulu: Tikulowera kuti?
Wolemba:
Joseph KAYIRA
atatha zaka 58 dziko la Malawi litalandira ufulu wodzilamulira kuchokera ku dziko la Britain, Amalawi ambiri adakali osauka, chuma cha Malawi sichikuyendabe bwino ndipo katangale wayanga ndele. Funso nkumati, tikulowera kuti? Ufulu wathu watipindulira?
Munthu wa zaka 58 ndi wamkulu ndithu; pa banja akhoza kukhala ndi ana ndi azukulu. Akhoza kukhala kuti anamanga nyumba, ali ndi munda, chuma komanso akukhala umoyo wabwino.
Pa zaka 58, dziko la Malawi liri ngati munthu amene zake sizikuyenda. Malawi ali ngati munthu amene anabadwira mu banja lomwe sitinganene kuti linali losaukitsitsa koma lija chakudya chimapezeka, makolo amatha kutumiza ana ku sukulu komanso mwai wokhala ndi katundu wofunikira pa banjapo unalipo.
Mwanayo — Malawi — anali ndi mwai wopita patali ndi maphunziro ake ndipo anapita ku sukulu yaukachenjede komwe anakachita maphunziro apamwamba. Mwanayo anachita mwai ndithu mpaka kukapitiriza maphunziro ake ku sukulu zapamwamba zaukachenjede. Atabwera kumeneko – mwanayo anadzayamba ntchito yapamwamba m’boma. Anakakhala ku likulu la dziko lino ku Zomba ndipo likululi litasamukira ku Lilongwe iye anakakhala ku Lilongwe.
Koma atayamba ntchito ama-ngosakaza ndalama zake pa zinthu zosadziwika ndipo umoyo wake wakhala usakuyenda bwino mpaka lero. Chonsecho mwanayo amalandira ndalama zambiri ndithu zoti atha kudyetsa banja lake kuyambira pa 1 kufika pa 30. Sakwanitsa kuchita zambiri. Pa zaka 58, akukhala ngati wangoyamba kumene ntchito. Umutu ndi m’mene ziliri ndi dziko la Malawi.
Ulamuliro wa chipani chimodzi
Pulezidenti woyamba wa dziko lino Ngwazi Dr Hastings Kamuzu Banda anali ndi kufuna kwabwino kuti dziko la Malawi likhale lotukuka, lodzidalira pa chuma komanso lomwe anthu ake ali ndi chakudya chokwanira. Kuchokera mchaka ch 1964, uthenga wa Kamuzu unali woti: anthu ake akhale ndi chakudya chokwanira, akhale ndi zovala komanso agone mu nyumba zosadontha mvula ikamagwa.
Amalawi analimbikitsidwa kugwira ntchito molimbika m’minda yawo podzala mbewu zosiyanasiyana monga chimanga, mtedza, thonje, tiyi komanso fodya. Cholinga cha Kamuzu chinali choti alimi azitha kukhala ndi chakudya chokwanira komanso akhale ndi ndalama akagulitsa mbewu zawo mu misika yomwe anakhazikitsa pansi pa bungwe la Agriculture Development and Marketing Corporation (Admarc). Zinthu zinkayenda ndithu ndipo dziko la Malawi chuma chake chimayenda bwino.
Kamuzu anayamba kutukula dziko la Malawi pomanga zinthu zosiyanasiyana monga sukulu, miseu, zipatala ndi zina. Kamuzu anakhazikitsanso makampani ambiri omwe anathandiza kuchepetsa ulova. Makampaniwa amachita bwino ndipo potero chuma cha Malawi chimayendanso bwino.
M’mene Kamuzu ankachoka pa udindo wa mtsogoleri wa dziko lino mchaka cha 1994, zambiri zinali zili bwino. Chuma chinali chili bwino, miseu yambiri inali yaphula, sukulu zaukachenjede zimalandira ndalama zawo zoyendetsera maphunziro mosavuta ndipo m’boma m’mene munali kusunga mwambo pa nkhani yoyedetsa chuma cha boma.
Mwina mbali imene inavuta ku mbali ya Kamuzu inali yozunza anthu. Aliyense amene amaganiziridwa kuti akudana ndi ulamuliro wa Kamuzu amamangidwa. Anthu ambiri anakathera ku ndende chifukwa cholankhulapo pa nkhanza zimene akuluakulu andale, apolisi ndi ena ankachitira Amalawi.
Anthu ena anakakamizidwa kuchoka kuno ku Malawi kaamba ka nkhanza zomwe chipani cha Malawi Congress (MCP) chinkachitira anthu. Panali gulu la achinyamata a chipanichi la Youth League, lomwe linkapita m’midzi nkumaopzeza, kumenya kapena kulanda katundu wa Amalawi mu dzina la Kamuzu. Uku kunali kuwaphera ufulu Amalawi.
Gulu lina lovuta linali la polisi lapedera lotchedwa Special Branch. Gululi limanka limanga onse amene amaganiziridwa kuti akudana ndi ulamuliro wa Kamuzu. Anthu ambiri anathera ku ndende chifukwa cha gululi. Anthu ena anathawa m’dziko muno poopa nkhanza za MCP.
Kwa zaka makumi atatu (30) Amalawi anakhala pa ulamuliro wankhanza ndipo anthu ena olimba mtima analolera kuika mitu yawo pa njanji kuti athane ndi ulamuliro umenewu. Apa ndi pomwe kunabwera maganizo oti kukhale riferendamu, chisankho chapadera chofuna kumva maganizo a anthu ngati kunali koyenera kupitiriza ndi ulamuliro wa chipani chimodzi kapena kukhazikitsa ulamuliro wa zipani zambiri…
Subscribe Mkwaso news paper online and read the whole story.