MkwasoUncategorized

Chiona akufuna Flames

Wolemba:

Bartholomew BOAZ

Pempha ndipo udzalandira, gogoda ndipo chitseko udzatseguliridwa. Jack Chiona, wosewera pakati mu timu ya Dwangwa United, wapempha ndipo wagogoda ndipo kwatsala ndikoti khomo lophaphatiza la Flames litseguke kuti alowe. 

Chiona, yemwe waithandiza Dwangwa kuti ipulumuke mu mchokocho wa ligi ya chaka chino, wati akufunitsitsa kumenya mu timu ya dziko lino ya Flames.

“Khumbo langa ndilosewera mu Flames basi,” anatero Chiona. “Ndiyesetsa kulimbikira mpaka anthu omwe amasankha osewera a mu timuyi atandipatsa mwayi,” anaonjezera.

Chiona ndi wosewera pakati yekhayo amene wamwetsa zigoli zambiri mu ligi ya chaka chino. Iye wamwetsa zigoli khumi ndi zwiri (12).

Kwa iye ati kusewera mu Flames likhala ngati khwerero lopitira patali. “Ndimafunitsitsa kukasewera kunja kwa dziko lino,” watero Chiona, yemwe ankaphunzira pa koleji ya PACT.

Chiona adasewerapo mu timu ya Mponela United. Kenako adabwera ku Dwangwa United komwe anaithandiza kulowa mu ligi yayikulu kuchoka mu ligi yaying’ono ya Chipiku.

Iye anati ndiwokondwa kuti waithandiza timu ya Dwangwa kukhazikika mu ligi yayikulu ya TNM.