ZOPANDA PAKE: Zounika Pulezidenti m’masiku 100 n’zosapindulitsa
Wolemba: Precious MSOSA
Chizolowezi chomawunika momwe Pulezidenti wachitira m’masiku ake 100 oyambirira chikhalireni pampando ati ndichopanda pake chifukwa ati sizingatheke kuti ku Malawi Pulezidenti apange zinthu zolozeka m’masiku amenewa.
Posachedwapa, Pulezidenti Dr Lazarus Chakwera wachipni cha Malawi Congress (MCP) ndipo adatsogolera Mgwirizano wa Tonse pachisankho chatso-pano cha pa 23 Juni chaka chino, adakwanitsa masiku 100 chitengereni mpando kuchoka kwa a Peter Mutharika achipani cha Democratic Progressive (DPP).
A Chakwera adatchula zinthu 35 zimene adati azichita mu masiku 100 amenewa monga ulamuliro wabwino, kuthana ndi katangale, kukhazikitsa utsogoleri wautumiki, kulimbikitsa kuchita zinthu poyera m’boma ndi kukhazikitsa lamulo loti anthu azipeza nkhani mosavuta mwa zina.
Koma ena ati zimenezi si zinthu zoti mpaka nkumaima pachulu kumazikamba chifukwa ati sizomwe adalonjeza pankhani ya misonkhano yokopa anthu. Ena akuti a Chakwera alephera kutukula amayi monga momwe adalonjezera panthawi ya kampeni.
Mkulu wa bungwe la Think Tank a Ken Msonda anati ngakhale ndikoyenera kumatsanzira zinthu zina kuchokera ku maiko ena, ganizo lotengera kuwona momwe Pulezidenti wagwirira ntchito m’masiku 100 wati ndilosagwira kwenikweni m’dziko mwathu muno.
“Kwathu kuno ganizo lomaona momwe Pulezidenti wayambira ntchito m’masiku 100 oyambirira ndilosagwira kwenikweni chifukwa sizingatheke mtsogoleri kuchita chinthu cholozeka m’masiku amenewa chifukwa cha zinthu zambiri zomwe mwa izo ndi umphawi,” anatero a Msonda.
Koma mmodzi mwa akatswiri olankhula pankhani zandale a Ernest Thindwa wati kuwunika momwe Pulezidenti wachitira m’masiku 100 oyambirira zitha kutengera ndi magawo omwe pulezidentiyo akuwunikidwa.
“Mwa chitsanzo pali zina zoti zitha kuchitika mu nthawi yochepa komanso zina zoti zitha kuchitika mu nthawi yayitali kotero zitha kutengera kuti mtsogoleriyo akuwunikiridwa zinthu zochitika mu nthawi yayitali bwanji,” anatero a Thindwa.
Chikhalidwe chomawunika mo-mwe mtsogoleri wagwirira ntchito m’masiku 100 oyambirira mu ofesi yake atangosankhidwa chidayamba ndi mtsogoleri wakale wa dziko la America a Franklin Delano Roosevelt m’chaka cha 1933 ndipo ku Malawi kuno zinayamba ndi malemu Bingu wa Mutharika.