Manoma mchipululu… sinthawi yolozana dzala
Wolemba: Precious MSOSA
Pamene mamulumuzana a timu ya Mighty Wanderers adakasinkhasinkha zamomwe angapitire chitsogolo kampani yogulitsa galimoto ya m’dziko la Japan ya Be Forward itasiya kuwathandiza, akuluakuluwa alowanso mkachipinda komata kufuna kudziwa chomwe chagwera timuyi kuti isamachite bwino mmasewero ake.
Chiyambireni TNM Supa Ligi ya 2020/21, Wanderers yapambanako mase-wero amodzi mwa masewero pafupifupi asanu ndi amodzi. Timuyi inagonjetsa TN Stars 3-1 ndikufanana mphamvu ndi matimu monga Mzuzu Warriors 1-1, Silver Strikers 0-0 ndipo inagonja kwa Karonga United 2-0 komanso Mafco 1-0.
Kutsatira kusachita bwinoku, komiti yoyendetsa timuyi motsogozedwa ndi mlembi wamkulu a Victor Maunde apereka masewero atatu oti aphunzitsi a timuyi apulumutse ntchito zawo. A Bob Mpi-nganjira ndi a Oscar Kaunda ndiomwe amaphunzitsa timuyi.
Nawo otsatira timuyi ataya kale chikhulupiliro pamene anapita pa tsamba la mchezo la timuyi ndikuyisambwaza.
Kusapambana kwa timuyi kukuyembekezeka kukhudzanso kwambiri chikonzero chomwe akulu akulu a timuyi anakonza ngati njira imodzi yopezera ndalama pamene timuyi yasanduka ya masiye. Mchikonzerochi chomwe akuyembekezeka kupeza ndalama zosachepera K1 miliyoni, otsatira timuyi akupemphedwa kumatumiza K100 kudzera pa lamya ya mmanja.
Koma malingana ndi ena mwa ochemerera timuyi omwe analemba pa tsamba la mchezoli, ena akuti saperekanso ndalamayi mpaka itayamba kuchita bwino.
A Morris Phiri anati: “Mukadzayiona ndalama yanganso mudzandifunse.” Nawonso a Sire Emreys Centurion Storleys anati “Simudzayionanso K100 yanga. Ndatopa kufupa zosavina.”
Timuyi italepherana ndi Chitipa United masabata awiri apitawo, ochemerera ena anayankhulitsana mau osakhala bwino ndi kaputeni wa timuyi Alfred Manyozo ngakhale iye anapepesa patapita masiku angapo.
Koma poyankhulapo pa mmene zinthu zikuyendera ku Lali Lubani, wapampando wa timuyi a Symon Sikwese anati iyi sinthawi yolozana zala ndipo mmalo mwake banja la nyerere likuyenera kubwera pamodzi ndikuona momwe angatulukire mu zovutazi.