Kukhala chete kwa mabungwe a Public Affairs Committee (PAC), mabungwe amipingo ndi mabungwe omwe siaboma – Civil Society Organizations (CSOs) – pa nkhani za ndale zomwe zikuchitika m’dziko muno kukudabwitsa nzika za Malawi.
M’busa wa mpingo wa CCMIPD, a Harold Kachepatsonga, alembera chikalata mabungwewa pa nkhani yosayankhulako pa m’mene dziko lino likuyendera – maka pa chuma, kusowa kwa mafuta, njala, kuzimazima kwa magetsi ndi kukwera mtengo kwa zinthu tsiku ndi tsiku – zomwe zikuika Amalawi pa mavuto adzaoneni.
Zimabweretsa chilimbikitso pakati pa anthu mabungwe omwe siaboma mukalankhulapo pamene zinthu sizikuyenda bwino. Inu mumalimbikitsa umodzi komanso mtendere. Mumamenyera anthu maufulu osiyanasiyana koma mukakhala chete zinthu zikamasokonekera mumapereka chiopsezo pa ulamuliro wa demokalase,” yatero kalata yomwe walemba m’busa Kachepatsonga.
Mwa zina, a Kachepatsonga apempha mabungwewa kuti agwiritse njira zawo zofalitsira uthenga komanso kuwuza boma kuti lizichita zinthu zake poyera. Iwo akuti boma liyenera kupeza njira zokhazikika zothana ndi mavuto omwe ayanga ndele m’dziko muno. Mwa zina iwo akuti akuluakulu a boma achite chotheka pokumana ndi anthu akumudzi, ndi kumva mavuto awo ndi kupeza njira zowathetsera.
“Lolani anthu achite ziwonetsero mwa bata zomwe zimawonetsa kuti demokalase ilipo m’dziko chifukwa ndi njira yokhayo yomwe anthu amatulira madando awo kwa adindo omwe sangawafikire paokha. Utsogoleri wanu ndi mphamvu zanu ndi zomwe zikufunika nthawi ino yomwe anthu akukumana ndi mavuto. Tiyeni tigwirane manja polimbikitsa mfundo za demokalase yathu kuti Malawi akhale okomera tonse,” atero a Kachepatsonga.
A Kachepatsonga ati chomwe chawakhudza kwambiri nkusayankhula kwa mabungwewa pa nkhani zomwe zikuchitika, pamene mabungwewa ali ndi udindo wowunikira boma pomwe zinthu sizikuyenda bwino komanso kulankhula pomwe maufulu a anthu akuphwanyidwa
Iwo ati akukhulupilira kuti mabungwewa ali ndi mphamvu yoyankhula mwa ukadaulo pa nkhani za chuma ndi ulamuliro wabwino.
“Koma kukhala chete kwawo kukudabwitsa anthu omwe amawakhulupirira. Cholinga cha kalatayi nkufuna kuti mabungwewa adzuke nkuyankhulapo pa zomwe zikupsinja Amalawi. Ndili ndi chikhulupiriro kuti akawona mavuto omwe alipowa, titha kukhala ndi yankho labwino kuchokera kwa adindo anthu lokhudza mavuto omwe Amalawi akukumana nawo,” atero a Kachepatsonga