Dalayivala amumanga atanyamula anthu ochuluka
Apolisi ku Lilongwe amanga dalaivala wa minibasi, a Thomson Bisayi, a zaka 35, atapezeka atanyamula anthu 37 mu minibasi yomwe imayenera kunyamula anthu 16.Malingana ndi m’neneri wa polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, apolisi alandanso minibasiyo yomwe ndi Toyota Hiace, MH 10964.
A Chigalu ati minibasiyi imachoka msewu wa Santhe ndipo imalowa mtauni ya Lilongwe nthawi ya m’mawa wa lero mma 3 koloko.Kupatulapo kunyamula anthu ochuluka chomwecho, minibasiyi, malinga ndi a Chigalu, inanyamulanso matumba a chimanga mopitirira – zomwe zaika anthu pachiopsezo.
“Apolisi owona za pansewu atayimitsa minibasiyi pa malo a chipikisheni a ARET, anachita jenkha kuona khwimbi lomwe linali mu minibasiyo. Anthu ena anaimirira pomwe ena anakhala mopanikizika. Nthawi yomweyo apolisiwa anatsitsa anthuwo ndipo anamanga Bisayi ndi kulanda minibisiyo,” anatero a Chigalu.
Apolisi akupempha anthu okwera magalimoto kuti nawo ali ndi udindo othandizira apolisi pokana m’chitidwe wokwera anthu ochuluka kuti achepetse ngozi za pa nsewu. Iwo ati anthu adziwona kuti galimoto yomwe akukwera ili ndi zoyenereza poteteza miyoyo yawo.
A Bisayi amachokera m’mudzi mwa Gamba, Mfumu yayikulu Chilooko, m’boma la Ntchisi.