Ayankhulapo za momwe achifwamba anatenthera Montfort Print mu1992
Wolemba: Joseph KAYIRA
A Frank Winiko, amalongosola bwino kwambiri m’mene anthu otsatira chipani cha Malawi Kongiresi (MCP) anachitira chiwembu malo osindikizira mabuku a Montfort Print – monga m’mene amadziwikira nthawi imeneyo – pa 19 Malichi mchaka cha 1992 – ku Balaka. A Frank omwe mpaka lero akutumikirabe kunyumba ya anse-mbe ku Montfort Media ku Balaka akuti chikhulupiriro chawo pa chipembezo chinazama kwambiri atapulumuka ku imfa pa tsikulo.
“Anthu achiwembuwa anali opanda chisoni ndipo anatiuziratu kuti tsiku lathu lomaliza pa dziko lapansi linali limenelo. Anali atanyamula zida monga nkhwangwa, zikwanje ndi zida zina zoopsa.
“Iwowa anali atapsa mtima ndi kalata yomwe aepiskopi ampingo wa katolika analemba m’chaka cha 1992 yotchedwa ‘Kukhala M’chikhulupiriro Chathu’(Living Our Faith). Monga mukudziwa kalata imene ija inawasokoneza kwambiri a Kongiresi ndipo anayamba kusaka malo amene kunasindikizidwa kalatayo kuti akaonongeko,” anatero a Frank.
Kalatayi inali itawerengedwa Lamulungu pa 8 Malichi 1992 m’matchalichi onse a Mpingo wa Katolika muno mu Malawi. Mwa zina kalatayo inkadzudzula zolakwika zomwe boma la Pulezidenti Ngwazi Dr Hastings Kamuzu Banda linkachitira Amalawi. Aka kanali koyamba kuti munthu, mpingo kapena bungwe libwere poyera nkudzudzula zolakwika zomwe mtsogoleriyu, yemwe ankaopedwa kwambiri panthawiyo ankachita.
Izi ndi zomwe zinachititsa kuti anthu otsatira chipanichi aganize zopita ku Balaka nkukachitira chiwembu malo omwe kuna sindikizidwa kalatayi, omwe panthawiyo ankawatchula kuti Montfort Print. Kumeneko, Bambo Piergiorgio Gamba ndi amene ankayang’anira malowa ndi ansembe ena ochokera m’dziko la Italy. Ku Lilongwe akuluakulu a chipani cha MCP anasonkhananso ku likulu la chipanichi komwe adakambirana zofuna kunyonga mabishopu a Mpingo wa Katalolika.
A Frank akuti tsiku la chiwembulo anaweruka kuncthito cha mma 8 koloko madzulo monga amachitira nthawi zonse. Atafika panyumba yawo, yomwe siinali patali kwenikweni ndi komwe amakhala a nsembe komanso komwe kunali makina osindikiza mabuku, anamva kuitana. Kuti ayang’ane anaona akamuna ochuluka ndithu – mwina khumi kapena kuposera apo.
Atalonjerana nawo, anthuwo anawapempha kuti awaperekeze komwe kunali makina osindikiza mabuku kaamba koti iwo sankadziwako. A Frank atanyinyirika kuti aweluka kale ndipo analibe malingaliro obwereranso ku ntchitoko, anthuwo anawasimikizira kuti sakachedwa kaamba koti ntchito yawo inali yongokawawonetsa kumaloko.
Monsemo nkuti achiwembuwa atabisa zida zomwe amakachitira upandu. Zinthu zinazayamba kusintha pomwe a Frank analondolera anthuwa mpaka pa geti lolowera kunyumba ya ansembe, komwenso kunali makina odindira mabuku ndi zina.
“Atangotitsegulira pa chipata ndinadabwa kuona kuti alonda anayi amene anali pamenepo, agwidwa ndi achiwembuwo. Mlonda aliyense anagwidwa ndi anthu awiri. Ineso ndinapezeka ndili m’manja mwa achiwembuwo. Kuti ndilankhuleko anandiwopseza kuti athana nane.
“Anzanga aja omwe anali a Chikuse, a Chauluka, a Luciano Malondera (Phiri) komanso a Kakhobwe, anatulutsa mawu oti; ‘Kodi a Frank mumatibweretsera chiwembu m’mene mumati tikutsegulireni?’ Ine ndinangoti nane ndikudabwa ndi zomwe zinkachitikazo. Apa ndipamene ndinaona kuti anthuwo anali ndi zida zoopsa. Chinanso chimene chinandidabwitsa linali fungo la mafuta a galimoto a petulo. Ndinadziwiratu kuti anthuwa sanabwere kudzacheza,” anatero a Frank.
Iwo akuti ali paulendo wa ku makina osindikiza mabuku achiwe-mbuwo anawamenya a Chikuse mmaondo ndipo mkuluyo anagwa pansi. Pokhala kuti achiwembuwo amafuna zamsangamsanga, iwo sanafune zoti awadzutse a Chikuse kuti akafike nawo komwe kunali makina osindikizira mabuku kuja.
Atafika kumeneko akuti achiwembuwo ankafuna kuti m’modzi wa ogwidwawo aphwanye chitseko nkulowa nkukawatsegulira koma anthuwa anakana. Achiwembuwo sanachedwe koma kuthyola ndi nkhwangwa chitsekocho.
“Ine nditaona kuti cholinga chawo chinali kukaotcha makina osindikiza mabukuwo, ndinawa-onetsa makina ena a fotokope omwe anali ovindikira ndi nsalu. Pemenepo wamkulu wa achiwembu aja analamula kuti awaze petulo makinawo. Analamulanso kuti akamaliza kuwaza petulo makinawo atiwazenso ife ndikutitenthera limodzi.

Frank kuloza nyumba yomwe panthawiyo munali makina osindikiza mabuku omwe anatenthedwa ndi aupandu (Chithunzi: Joseph Kayira)
“Ndinayamba kulira koma anthuwo sanawonetse chisoni chilichonse. M’menemo nkuti m’modzi wa ife, a Luciano Malondera Phiri anali atathawa. Anapeza mpata m’mene tinkalowa mu nyumbayi ndipo anakatulukira khomo lakuseri. Wotsalafe anatikakamira kuti tipsere limodzi ndi makinawo,” anatero a Frank.
Mkuluyu akuti mwai wothawa unazapezeka kaamba koti panali kusamvana pa momwe amayenera kutenthera makinawo. M’modzi wa aupanduwa anaponya msanga ma-chesi anzake akadali mkati mwa nyu-mbayo ndi ogwidwawo.
“M’mene amadzati mayo tifera momuno waponya msanga moto, mpamene nafe timathawa. Motowo anali atauponyera pa dzenera. Posakhalitsa anthu anayamba kutulukira chifukwa zinamveka kuti kwa ansembe kwabwera anthu aupandu. Ena mwa amene anafika mwaunyinji anali ana apa St Charles Lwanga Secondary School. Awa ndi amene anachita chotheka kuthana ndi ena mwa amene anadzachita chiwembu, kuphatikizapo mkulu wawo,” anatero a Frank.
Iwo akuti m’mene apolisi amafika nkuti moto utakolera ndipo anthu anachita chotheka kuuzimitsa. Mkuluyu anati anthu anali okwiya ndi apolisi kaamba koti anthu ankati amatumikira boma la MCP ndipo kubwera kwawo sikunali kozathandiza kukonza zinthu kweni-kweni.
“Chifukwa cha chisokonezo chomwe chinabuka, wapolisi m’modzi anagendedwa m’mutu nkugwa pansi. Anthu anali okwiya kwambiri kuti a MCP analeke-reredwa mpaka kudzawotcha malo a Montfort chifukwa chosindikiza kalata ya mabishopu.
“M’modzi wa achifwambawo anagwidwa ndi gulu la anthu atalephera kuwawopseza ndi zida zomwe anali nazo. Anamenyedwa mpaka thapsya. Panali ena omwe ankafuna kungomuphwanya ndi mwala m’mutu wogwidwayo koma ansembe ndi ena anathandizira kule-tsetsa,” anatero a Frank.
Anthu anadzabalalika nkuyamba kuthawa atamva kuti kwabwera ‘asilikali’ a mfuti omwe sankanyengerera powombera. M’mene kumacha m’mwa nkuti kumaloko kuli masilipasi a mitundu yosiyanasiyana, ambiri ambali imodzi, omwe achinyamata ndi anthu a m’mudzi anasiya pothawa asilikaliwo.
Mkuluyu akuti amati akalingalira m’mene zinalili pa tsikulo, ndi chifundo cha Mulungu kuti ali moyo mpaka lero. Iye akuti anthu amene anabwera kuzachita zaupanduwo “anabwera kudzapha ndi kuononga.”
“Achifwambawotu anali anthu opanda chisoni. Kuwona zida zimene ananyamula mpamene umazindikira kuti anthuwa zinali zigawenga zenizeni. Ife tili moyo chifukwa cha chikondi ndi mphamvu ya Mulungu. Cholinga chawo amafuna kuti ife tifere momwe munali mashini mo koma Mulungu anatiteteza,” anatero a Frank.
A Frank anati ulamuliro wa Kongiresi ya nthawi imeneyo unali woopsa, wosalemekeza umoyo wa munthu ndipo kwa ambiri amene amatumikira mchipanichi, zaupandu chinali chikhalidwe chawo.
Iwo akuti panalibe chifukwa chotenthera makina osindikiza mabuku chifukwa cha kalata ya Aepiskopi. Komanso panalibe chifukwa chovulazira anthu mpaka kufuna kuwatentha ndi moto chifukwa choti amagwira ntchito kumalo amene kalatayo inasindikizidwa.
A Frank akuthokoza kuti ngakhale anakumana ndi zokhoma mu ulamuliro wa chipani chimodzi, pano kuli demokalase ndipo anthu akukhala mwaufulu. Mkuluyu wati Amalawi akuyenera kuteteza demokalaseyi kuti ulamuliro wa nkhanza usadzabwererenso. “Kwa amene tinaona m’mene zifwamba za chipani zinkachitira nthawi imeneyo, sitingalorerenso kuti tibwerere ku ulamuliro wa chipani chimodzi. Sitifunanso kubwerera mu nyengo za anthu amene anazatitenthera mashini,” anatero a Frank.
