Apatsidwa zaka 13 chifukwa chogwiririra mwana
Wolemba: Precious MSOSA
Bwalo la milandu la Liwonde lomwe limakumanirana kwa Phalula m’boma la Balaka lagamula a Felix Joseph kuka-gwira ukaidi kwa zaka 12 chifukwa chogwiririra mwana wa zaka 12.
Wofalitsa nkhani m’bomali a Felix Misomali anati woimira boma pa milandu a Liston Sabola, anauza bwalolo kuti a Joseph anapalamula mlanduwu mwezi wa Januwale chaka chino pomwe mwanayu anatumidwa ku chigayo komwe iwo ankagwirako ntchito ngati wogayitsa.
A Sabola anapitiriza kuuza bwalolo kuti mwanayu atafika, bamboyu adamunyengerera kuti agonanane naye koma anakana mpaka mkuluyu anangomukokera mu chimodzi mwa zipinda pa malopo. Iwo anati bamboyu anakwa-nitsa kupanga khalidweli katatu ndipo ulendo uliwonse amamupatsa K500.
“Koma pa tsiku la chitatu pomwe panali pa 26 Sepitembala, mwanayu anachucha magazi ndipo izi zinamuchititsa kukawulula kwa adzakhali ake omwe nawonso anakatula nkhaniyi ku polisi ya Phalula,” anatero a Sabola.
Koma atakawonekera ku khoti, a Joseph anaukana mlanduwo kotero mboni zinayitanidwa mpaka iwo anapezeka wolakwa.
Popereka chigamulochawo, woze-nga mlanduwo a Jones Masula anagwirizana ndi boma kuti apereke chilango chokhwima choncho iwo anakhazikika pa zaka 13.
A Joseph amachokera m’mudzi wa Mthengomwacha, Mfumu Yayikulu Chanthunya m’boma la Balaka.
Pakadalipano apolisi m’bomali akupempha makolo kuti adzitsatira bwino ana awo ngati njira imodzi yowateteza.