Chinyengo chakula m’misika ya Adimaki
Wolemba: Precious MSOSA
Pamene njala ikupitiriza kusautsa anthu ambiri m’madera osiyanasiyana m’dziko muno, anthu ena m’boma la Balaka adandaula chinyengo chomwe ati chilipo pa kagulitsidwe ka chimanga m’misika yomwe nthambi la Admarc latsegula.
Boma la Balaka ndi limodzi mwa maboma omwe ali ndi chiwerengero chochuluka cha anthu omwe akusoweka chakudya, malingana ndi lipoti latsopano lomwe komiti ya Malawi Vulnerability Assessment Committee (Mvac) linatulutsa m’mwezi wa Disembala chaka chatha. Maboma ena ndi monga Neno komanso Nsanje.
A Esnart Chimpere, a m’mudzi wa Kanyumbayaka, Mfumu Yayikulu Sawali anauza nyuzipepalayi kuti m’madera ambiri omwe nthambiyi yatsegula misika zinthu sizikuyenda bwino.
Mwa chitsanzo, iwo anatchula pa msika wa ku Laimu komwe anati nthawi zambiri anthu ena akumangobwerera osagula chimanga chifukwa pakumangodzadza mavenda.
Kuwonjezera apo, a Chimpere anatinso a komiti yomwe ndi ya anthu am’mudzi nawo sakuyendetsa bwino ntchitoyi kwenikweni chifukwa amazikondera okha.
“Zoti anatitsegulira msika sizikuwonekanso chifukwa mavenda ndi atsogoleri ndiomwe akumakhala patsogolo kukolezera chinyengo. Mamembala ena akomiti akumalandira ndalama kuchokera kwa mavenda kuti anthu awo agulitsidwe chimanga,” anatero a Chimpere.
Koma wapampando wa komiti ya pa msikawu a Felix Namboya anati nkhani za chinyengo zinalipo ndi komiti yakale ndipo chiyambireni utsogoleri wawo zinthu zayamba kumayenda bwino.
“Dziwani kuti komiti yomwe ndikutsogolera yangosankhidwa kumene chifukwa yomwe inalipo anthu sanali nayo chikhulupiriro chifukwa cha nkhani za chinyengo,” anatero a Namboya.
Malingana ndi anthu pa msikawo, chomwe chikumachitika ndichakuti nthumwi za mavenda zikagula chimangacho, izo zikumakakhala pena pake ndikumakachipakira pamodzi ndikukwezetsa njinga.
Poyankhapo pa khalidweli, a Namboya anati ichi ndi chifukwa mamembala ena a komitiyi akumazungulira pa malopa ndipo akawona izi akumalanda chimangacho.
Koma mkuluyu anapempha akuluakulu a Admarc kuti aganizire zowonjezera chimanga chomwe amatumiza kaamba koti anthu ochokera madera ena akumafikanso ku msikawu.
Wamkulu woyang’anira misikayi m’bomali a Samuel Kafumbula anati iwo sanalandirepo madandaulo aliwonse. Iwo anati kukhazikitsidwa kwa makomiti m’misikayi ndikufuna kuchepetsa mavuto ngati amenewa ndipo ngati izi sizikusintha kanthu, a komitiyo ndiye kuti alinso mu gulumo.
Koma iwo anatsimikizira anthu kuti zowonjezera mlingo wa chimanga womwe amagulitsa pa tsiku aziganizira chifukwa ndi dandaulo lochokera m’misika yambiri. Anthu pafupifupi 1.9 miliyoni ndiomwe asowekere chakudya pa nthawi ino mpaka kudzafikira kukolola, malingana ndi lipoti latsopano la Mvac.