MkwasoUncategorized

Chimulirenji wapempha anthu asamukire kumtunda

Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Everton Herbert Chimulirenji wapempha anthu omwe akukhala m’madera omwe kumakonda kusefukira madzi kuti asamuke kupita kumtunda ngati njira imodzi yochepetsa mavuto angozi zogwa mwadzidzidzi.

Iwo anayankhula izi m’boma la Ntcheu pa sukulu ya Dimba, Mfumu Yayikulu Masasa poyendera mabanja omwe adakhudzidwa ndi ngozi ya madzi m’derali. Wachiwiri kwa mtsogoleriyu anati madela omwe anthu ambiri amakhala amadziwa kuti ndi ovuta maka nyengo ino ya mvula azionetsetsa kuti achokako kupita ku mtunda osati kukhalabe komweko.

Chimulirenji: Osakakamira malo omwe akukupezetsani mavuto

“Tsoka sasimba. Tsiku lina tidza-bwera pano ndi chisoni madzi atapha achibale anthu ndi kutivulaza kumene. Kupewa zimenezi tikuyenera kusamukira ku mtunda kuti tichepetse mavutowa osati kukakamira chifukwa ndi malo amakolo athu,” anatero a Chimulirenji.

Iwo anapempha anthuwa kuti adzale mitengo chifukwa malo ambiri ndi opanda mitengo zomwe zikuchititsa madzi kupeza njira zowonongera mbewu zawo ndi katundu. 

Phungu woyima payekha wa m’derali Nancy Chiola-Mdooko ana-pempha boma kuti liwaganizire powamangira mgula omwe madzi adzitha kuyendamo osafika kumanyumba anthu.

“Ndikupempha boma kuti litiganizire mgula kuno chifukwa ngati sitimanga mgula chaka chilichonse mudzibwera kuno kudzathandiza anthu omwe akhudzidwa ndi vutoli,” anatero a Mdooko.

A Mdooko anathokoza boma powathandiza anthu ake mwachangu omwe anakhudzidwa ndi ngoziyi pa 2 Januwale. Mabanja   okwana 252 ndi omwe anakhudzidwa ndipo mabanja 63 akusowa pokhala kaamba koti nyumba zawo zinagwa ndipo pakadali pano akukhala pa sukulu ya Dimba zomwe zachititsanso maphunziro kusokonekera.