Uncategorized

Idzani kwa ife… NAM, FDH imema makampani kuthandiza mpira wa manja

Wolemba: Precious MSOSA

Bungwe loyang’anira mase-wero a mpira wa manja m’dziko muno la Netball Association of Malawi (NAM) komanso banki ya FDH yomwe ikuthandiza ligi ya masewerowa apempha makampani komanso ochita malonda kuti aganizireko zothandiza masewerowa.

Mtsogoleri wa NAM a Vitumbiko Gubuduza ati pakadali pano matimu ambiri mu ligiyi alibe makampani owathandiza zomwe zikuchititsa kuti masewerowa asamapite patsogolo kaamba koti osewera sayikapo chidwi.

Poyankhula pa mapeto pa ligi ya FDH ku bwalo la KUHeS mu mzinda wa Blantyre, a Gubuduza anati ichi ndi chifukwa akupempha boma kuti liganizire zoyika chikonzero cha padera ku makampani omwe angabwere po-yera kuthandizira matimuwa.

“Mwachitsanzo, boma litha kupereka misonkho yofewerapo ku makampani omwe akuthandiza masewerowa kapena matimu chifukwa pamene makampaniwa akutero, iwo akuthandiziranso boma kumbali yotukula masewerowa komanso kupereka chochita kwa atsikana ambiri omwe amatengapo gawo pa mpirawu,” anatero a Gubuduza.

Iwo anati mwa matimu 12 mu ligi ya mpira wa manja ya FDH, asanu ndi imodzi ndiomwe akuthandizidwa ndipo kuti mwa matimuwa, anayi akuthandizidwa ndi boma kudzera mu nthambi zake zosiyanasiyana pomwe awiri ndiomwe akuthandi-zidwa ndi ena.

Timu ya Blue Eagles ndiyomwe inatenga ukatswiri wa ligi ya FDH

Matimu anayi omwe amatha-ndizidwa ndi boma ndi monga Blue Eagles yomwe ikuthandizidwa ndi nthambi ya polisi, Civonets yomwe ikuthandizidwa ndi ofesi ya Pulezidenti ndi nduna (OPC), Prison Queens yomwe ikuthandizidwa ndi nthambi ya ndende komanso MAFCO soldiers yomwe imathandizidwa ndi nthambi ya asirikali a ku Salima. 

“Tili ndi mwayi kuti a FDH akumathandiza matimu onse kuti akwanitse kuyenda ndi kusewera masewero a ligiyi koma kumbali yomachita zokonzekera mutha kuona kuti matimuwa akuvutika kwambiri. Kuti masewerowa apite patsogolo, matimuwa akumayenera kumakhala ndi zokonzekera zabwino chifukwa pa-kutero titha kumaona mpikisano wapamwamba kwambiri,” iwo anatero.

Mmodzi mwa akuluakulu a banki ya FDH a Noel Nkulichi anati anali odabwa kuti makampani komanso a malonda sanaonekere kwambiri mu ligiyi choncho ndichifukwa anati tsopano nthawi yakwana yoti maguluwa ayambe kukonda masewero a mpira wa manja.

Iwo anati masewerowa ali ndi kuthekera kochuluka kofikitsa mbiri ya dziko lino patali choncho ndikofunikira kuthandiza matimu omwe akusowekera thandizo.

Mlembi wa ligi ya masewero a manja ya Blantyre Urban a Anne Hanjahanja anati kuthandiza timu ya mpira wa manja sikulira zambiri kaamba koti zimafunikira ndi mayendedwe a osewera ku zokonzekera, madzi komanso chakudya pa nthawi ya mipikisano.

Poyankhapo pa za pempho la bungwe NAM, iwo anati pempholi labwera pa nthawi yake pomwe undunawu ukuwunikanso ndondomeko ya zamasewero kotero izi ziwunikiridwanso mu ndondomekoyi. 

Kusowekera kwa thandizo ku matimu ambiri ndikomwe kwachititsa chigawo cha kumwera kutaya ulamuliro wake pa masewerowa pamene chigawo cha pakati chatenga ufumuwu kudzera mu matimu monga Eagles, Civonets ndi Vanessa Sisters.