MkwasoUncategorized

Kufuna chilungamo: Ogwiriridwa kwa Msundwe akuona kuchedwa

Mabungwe akufuna chilungamo chioneke pa amayi wogwiriridwa

Wolemba: Joseph KAYIRA

Mpaka pano amayi ndi asungwana 17 omwe akuti anagwiriridwa ndi anthu omwe akuwaganizira kuti ndi apolisi kwa Msundwe, M’bwatalika, Kadziyo ndi Mpingu m’boma la Lilongwe akudikirabe tsiku lomwe anthu awupanduwa adzamangidwe ndipo boma liwapatse odandaula chipepeso monga mmene lipoti la bungwe lomenyera maufulu aanthu m’dziko muno linanenera.

Kugwiriridwa kwa amayi m’maderawa kukutsatira imfa ya wapolisi a Supuritendenti Usumani Imedi, yemwe anaphedwa ndi anthu ochita zionetsero kwa Msundwe m’boma la Lilongwe pa 8 Okotobala chaka chatha.

Malingana ndi malipoti a wailesi ndi manyuzipepala komanso kafukufuku yemwe anachita mabungwe omwe si aboma kuphatikizapo la Malawi Human Rights Commission (MHRC), apolisi atapita m’maderawa, anayamba kumenya ndi kuzunza anthu. Abambo ambiri anathawa m’makomo kusiya amayi ndi atsikana ndipo awa ndi omwe ana-gwiriridwa ndi anthu omwe akuwaganizira kuti anali apolisi.

Mpaka pano palibe wapolisi yemwe wamangidwa pomuganizira kuti anachita nawo zaupanduzi. Izi zadandaulitsa mabungwe ambiri omenyera ufulu wa amayi komanso maufulu ena osiyanasiyana.

Mkulu wa bungwe la NGO Gender Coordinating Network (NGO-GCN) Barbara Banda, anati ndi zodandaulitsa kuti mpaka pano apolisi sanamangebe anthu omwe anachita zaupandu kwa amayi ndi asungwana kwa Msundwe, M’bwa-talika ndi Mpingu.

“Zikukhala ngati nkhaniyi ndi yopanda pake chonsecho amayi ndi asungwana achichepere anagwiriridwa. Izi zinayika umoyo wa amayi ndi asungwana pa chiswe,” anatero a Banda omwe anali nawo pazionetsero zomwe bungwe la Huma Rights Defenders Coalition (HRDC) Lachinayi pa 9 Januwale 2020.

HRDC inakonza zionetserozo posakondwa ndi mmene apolisi akuyendetsera nkhani ya kugwi-riridwa kwa amayi ndi asungwana akwa Msundwe ndi Madera ozungulira. Iwo apereka nthawi yoti apolisi akhale atafufuza ndi kumanga oganiziridwa ngati mmene zimakhalira ndi anthu wamba oganiziridwa pamlandu.

Pa zionetsero za posachedwazi, HRDC inakapereka kalata yowonetsa kusakondwa kwawo ndi mmene zinthu zikuyendera pankhani yaku-gwiriridwa kwa amayi ndi atsikana kwa wachiwiri kwa mkulu wapolisi a John Nyondo.

Pa msonkhano wa atolankhani masiku apitawa, a Nyondo anafotokoza kuti kafukufuku woyamba wachitika ndipo ndicholinga cha apolisi kuti kafukufuku wachiwiri yemwe ali mkati wokhudza nkhaniyi athe msanga.

Polankhulapo za nkhaniyi pa wailesi ya Zodiak Broadcasting Station (ZBS) pa 12 Januwale chaka chino, mneneri wa apolisi a James Kadadzera anati ndi cholinga cha Malawi Police kuonetsetsa kuti chilungamo chichitike pankhaniyi.

Iwo anati kafukufuku wawo sakusiyana kwenikweni ndizomwe akafukufuku ena monga wa MHRC, NGO-GCN ndi zomwe atolankhani akhala akupeza.

“Chimene chikuchitika pakali pano ndichoti apolisi akufufuza mwakuya zolakwikazo kuti apeze anthu enieni omwe adachita izi. Akapeza umboni wokwanira atengera oganiziridwa ku khoti. Anthu adziwe kuti apolisi ali kumbali ya ophwanyiridwa ufulu choncho akuyenera kupeza umboni wokwanira asanatengere nkhaniyi ku khoti,” anatero a Kadadzera.

Wachiwiri kwa mkulu wa polisi a Nyondo (avala zakudawo) kulandira kalata ya madandaulo kuchokera ku mabungwe omwe siaboma

Pa tsiku lomwe apolisi ena akuganiziridwa kuti anagwirira amayi akuti kumalowa kudapita apolisi pafupifupi 100. A Kadadzera anena kuti si onse amene angaganiziridwe kuti anachita nawo zoipazo nchifukwa chake nkofunika kufufuza mozama kuti okhawo amene anaphwanya lamulo awatengere ku khoti.

Iwo ati ali ndi chikhulupiriro kuti pakutha pa sabata ziwiri kafukufuku wa apolisi akhala atafika kumapeto. Mneneri wa apolisiyu wapempha Amalawi kuti adekhe chifukwa zonse zikuyenda mwandondomeko.

Panamvekanso malipoti oti apolisi akuopseza amayi omwe akumakawafunsa mafunso okhudza kugwiriridwa ndipo nkhaniyi inakatulidwa ku bungwe la MHRC. Bungweli linakaitula nkhaniyi ku polisi. Koma apolisi anena kuti iwo ali ndi njira zimene amatsata pofunsa mafunso ndipo nkofunika kuti anthu agwirizane nawo kuti chilungamo chiyende ngati madzi.

A Tadala Peggy Chimkwedzule, omwe ndi pulezidenti wa bungwe la maloya achizimayi m’dziko muno la Women Lawyers Association nawo akuti kuchedwetsa kuyendetsa nkhaniyi kuti chilungamo chipezeke kukudandaulitsa amayi amene anagwiriridwa komanso Amalawi.

A Chinkwezule akuti pali maganizo otengera nkhaniyi ku khoti kaamba koti patapita miyezi itatu tsogolo la nkhaniyi silikuwoneka. 

“Nkhaniyi ndiyofunika kwambiri koma zimene zikuchitikazi zikuda-ndaulitsa chifukwa patatha miyezi itatu palibe chenicheni chimene chachitika. Kwa ife nthawi ndiyofunikira chifukwa amayiwa anawaphwanyira ufulu ndipo m’malo moti zinthuzi ziyende msanga tikuona kuti pali kuchedwa,” iwo anatero.

Iwo ati bungwe lawo liyesetsa kuti chilungamo chiwoneke pankhaniyi.

Malinga ndi zopeza za MHRC, amayi ena mabanja awo anasokonekera kaamba kogwiriridwaku, ena mabanja awo sakuyenda bwino pamene ena mpaka lero sakumvetsa kuti izi zinachitikiranji ndipo zasokoneza kaganizidwe kawo.

Ena akuti akulandira chitonzo chifukwa anthu amawaseka pamene ena akuti ndiokhumudwa kuti phungu wina wa Nyumba ya Malamulo a          Esther Kathumba anawajambula kanema pankhaniyi ndipo kanemayo pano ali ponseponse maka pa masamba a mchezo a WhatsApp.

Mwazina, bungwe la MHRC lati nkofunika kuti amayiwa athandizidwe powapatsa ndalama ya chipukuta misonzi komanso kuti anthuwa akuyenera kulandira uphungu wowathandiza kuti aiwale mavuto awo ndi kuyamba moyo wina watsopano.