Uncategorized

NKHONDO YA BOMA NDI HRDC YAVUTA

Pamene anthu ena amaganiza kuti Pulezidenti Peter Mutharika ndi bungwe lomenyera anthu maufulu la Human Rights Defenders Coalition akhala pansi nkupeza mayankho pakusemphana kwawo maganizo pa nkhani yoti wapampando wa bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), mayi Jane Ansah atule pansi udindo wawo, pano zadziwika kuti mtsogoleri wa dziko linoyu alibe maganizo wochotsa mayiwa pa udindo wawo.

Izi zipangitsa kuti mkangano wa mbali ziwirizi upitilire kaamba koti mabungwe alonjeza kuti apitiriza kuchita zionetsero mpaka mayi Ansah atule pansi udindo wawo ati kaamba kosayendetsa bwino chisankho cha pulezidenti pa Meyi 21.

Zionetsero zikamachitika anthu amaotcha zinthu

Pulezidenti Mutharika anauza wailesi ya British Broadcasting         Corporation (BBC) Lolemba pa 2 Sepitembala kuti sintchito yake kuchotsa mayi Ansah paudindo wawo. Mtsogoleri wa dziko linoyu anati ndiwodabwa kuti amabungwe ndi zipani zotsutsa boma akukakamira zochotsa mayi Ansah paudindo chonsecho anakatula nkhaniyi ku khoti kwinaku akuchitanso  zionetsero.

“Pali vuto chifukwa zipani zotsutsa kudzera mu bungwe la HRDC akukana kuvomereza zotsatira za chisankho. Anapita ku khoti ndipo mulandu kumeneko ndi woti khoti liwone ngati chisankho  chinayenda mwachilungamo kapena ayi. Wapampando pa nthawiyo anali a Jane Ansah. Panopa akuti atule pansi udindo wawo.

“Zionetsero zimene zikuchitikazi ndizofuna kuwakakamiza kuti atule pansi udindo wawo. Komanso m’mene akuchita zimenezi ali ku khoti kutsutsana ndi zomwe analengeza zokhuza chisankho. Apatu ndi pomwe mavuto akuya-mbira,” anatero a Mutharika pomwe anafunsidwa ndi wailesi ya BBC.

Pulezidenti Mutharika wanenetsa kuti sintchito yake kuwauza mayi Ansah kuti atule pansi udindo wawo chifukwa cha nkhani ya chisankho. A Mutharika akuti ndi zachidziwikire kuti chisankho chinachitika movomerezeka, mwamtendere ndi mwachilungamo.

“Mabungwe a European Union, African Union, Common Market for Eastern and Central Africa (Comesa)Southern African Development Community (SADC) ndi UNDP komanso boma la America anavomereza kuti chisankho  chinayenda bwino. Onsewa akuti chisankho chinali cha chilungamo. Ndiye ndiwauzirenji [mayi Ansah] kuti atule pansi udindo wawo?” anatero Pulezidenti Mutharika.

Pa nkhani yolunzanitsa Amalawi, a Mutharika akuti adikira kaye zotsatira za mulandu ku khoti. Iwo ananena kuti pakali pano kukambirana kwaya-mbika kale kuti mbali zotsutsana zimvane chimodzi.

Pa nkhani yokumana ndi zipani zotsutsa boma a Mutharika anena kuti akufuna kuti anthu amene akufuna kukambirana anene mwatchutchutchu mfundo za zokambiranazo. Mtsogoleriyu akuti adzaona ngati kuli          koyenera kuti adzakhale nawo pa zokambiranazo.

 Zipani zotsutsa ndi bungwe la HRDC akuti sizachilendo zomwe a Mutharika ayankha pa nkhaniyi.  Wapampando wa HRDC a Timothy Mtambo akuti a Mutharika akuyankha ngati sakudziwa zomwe zikuchitika m’dziko muno. Iwo ati mawu amene Pulezidenti Mutharika analankhula ndiwongofuna kubisa chilungamo.

A Mtambo anena kuti nthawi ino ndi yofunika kuti Pulezidenti Mutharika awonetse utsogoleri wake pomwe Amalawi ndi wokwiya ndi momwe zinthu zikuyendera.

“Iwo akuti adikira ajenda (agenda) asanavomere kuti achite zokambirana ndi wotsutsa boma pamene nthawi ino ndi imene dziko likuwasowa kuti awonetse utsogoleri wawo. Apa zikuonetseratu kuti sakudziwa zomwe zikuchitika mdziko muno,” anatero a Mtambo.

Mneneri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) m’busa Maurice Munthali akuti aliyense akudziwa momwe chisankho chinayendera kuti panali za chinyengo. Iye wati zomwe akuchita a HRDC ndi kulankhulira Amalawi omwe akufuna chilungamo chioneke.

“Zomwe zinachitika pa chisankho zinali zonyansa nchifukwa chake anthu akufuna Jane Ansah achoke pa mpando,” anatero a Munthali.

A Billy Mayaya, omwe ndi m’modzi wa akuluakulu omwe amakonza zionetsero ku HRDC akuti HRDC siitopa ndi zionetsero mpaka cholinga chawo chofuna kuchotsa pa mpando mayi Ansah chitatheka.

“Pa nkhani yokambirana ife ndiokonzeka kukambirana. Koma tikufuna kukambirana kukhale kwa chilungamo kothandiza kuti nkhani za chisankho ziyende bwino,” anatero a Mayaya.

Iwo akuti ndi cholinga cha HRDC kuona kuti zokambirana zoterezi zithandize kukonza Malawi komanso kudzamitsa demokalase.

Mphunzitsi wa ku sukulu yaukachenjede ya Chancellor a Ernest Thindwa ati nkofunika kukonza zinthu mwamsanga kuti dziko liyambenso kuyenda bwino.

Iwo ati chigamulo cha ku khoti chili ndi kuthekera kodzabweretsa          ziwawa ndipo nkofunika atsogoleri ayambiretu kukambirana kuti adzathe kuluzanitsa anthu panthawiyo.

“Atsogoleri ayambe kuunika kuti chikuvuta ndi chani kuti anthu           asemphane maganizo. Chofunika kuchita ndi chani? Kuunikira kotero kungathandize kuthetsa ziwawa,” anatero a Thindwa.

Mfumu ya achewa Kalonga Gawa Undi posachedwapa pa mwambo wa Kulamba ku Katete ku Zambia inati ndiyokhuzidwa ndi ziwawa zimene zikuchitika m’dziko muno. Iyo inapempha atsogoleri andale kuti        alolerane ndi kukambirana pa zomwe asemphanazo.

Bungwe la Public Affairs Committee (PAC) lakhala likukumana ndi          atsogoleri osiyanasiyana kuti pakhale zokambirana zodzetsa mtendere. Naye Pulezidenti wopuma a Bakili Muluzi akhala akukumana ndi andale komanso a HRDC pa nkhani ya mtendere.

Mtsogoleri wopuma wa dziko la Zambia a Banda nawo awonetsa chidwi chofuna kuluzanitsa mbali zonse zomwe zikukhuzidwa ndi nkhaniyi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *