Timaka? Flames ikumana ndi Burkina Faso
Wolemba: Bartholomew BOAZ
Itakhala miyezi yambiri isanasewere mu mpikisano waukulu Flames ikumana ndi Burkina Faso pa 12 Novembala ku Ouagadougou matimuwa asanakumanenso pa 16 Novembala chaka chino mu mpikisano wa AFCON.
Mphunzitsi wa Flames, Meck Mwase adaitana osewera okhalira m’dziko muno kuti akayambe zokonzekera.
Iye waitana Brighton Munthali (Silver Strikers), William Thole (Be Forward Wanderers) ndi Ernest Kakhobwe (Nyasa Big Bullets) ngati oima pagolo. Otchinga kumbuyo watenga Stanely Sanudi ndi Peter Cholopi (Wanderers), Gomezgani Chirwa, Precious Sambani ndi Nixon Nyasulu (Bullets), Paul Ndhlovu (MAFCO), Nickson Mwase (Civo Sporting) ndi Lusekero Malema (Karonga United).
Osewera pakati pali Chimango Kaira (Bullets), Chikoti Chirwa (Kamuzu Barracks), Rafik Namwera (Wanderers), Duncan Nyoni (Silver), Peter Banda ndi Chimwemwe Idana (Bullets), Isaac Kaliyati (Wanderers), Micium Mhone (Blue Eagles) ndiponso Lloyd Njaliwa (Moyale Barracks). Kutsogolo waitana Foster Beaton ndi Stain Dave (Silver) komanso Hassan Kajoke (Bullets).
Ambiri mwa anyamatawa ndiomwe adawagwiritsa ntchito pamene Flames imasewera masewero opimana mphamvu ndi Zambia komanso Zimbabwe. Flames idagonja ku Zambia ndi chigoli chimodzi kwa duu pomwe Zimbabwe itabwera matimuwa sanagoletsane chigoli.
Flames ili ndi phiri lalitali loyenera kukwera pa Burkina Faso, timu yomwe ili pa nambala 58 mumndandanda wa matimu padziko lonse. Burkina Faso idakhalapo yachiwiri pa mpikisano wa AFCON umene udachitika m’chaka cha 2013.
Kuonjezera apo, timuyi yaitana akatswiri pokonzekera masewero ake ndi Flames, ambiri mwa iwo akuse-wera kumaiko akunja kwa dzikolo. Mmodzi mwa iwo ndi monga wose-wera pakati Bertrand Traore amene pakalipano akusewera mu timu ya Aston Villa ku England.
Ena ndi monga goloboyi Kouakou Koffi amene akusewera ku Belgium, Steeve Yago (Caen, France), Issoufou Dayo (Morocco), Issa Kabore (France), Charles Kabore, yemwe ndi kaputeni, amasewera ku Russia, Abdou Traore (Turkey), Abdou Bandaogo (Spain), Cyrille Bayala (France) komanso yemwe wamwetsa zigoli ku timuyi Sibiri Traore (Morocco).
Koma Flames itha kuika chikhulupiriro chake mwa osewera monga Gabadinho Mhango (Orlando Pirates), Richard Mbulu, Gerald Phiri Junior (Baroka FC), Dennis Chembezi (Polokwane City), Chawanangwa Kaonga (Sporting Port Elizabeth) omwe ali ku South Africa. Schumaker Kuwali ndi John Banda (Songo, Mozambique) komanso Yamikani Chester (Las Vegas Light, America) ndi Charles Petro (Sherrif Tiraspol, Moldova).
Flames yakumana ndi Burkina Faso kokwana kanayi ndipo m’masewero onsewa siyinapa-mbanepo. Flames idagonja katatu ndi kufanana mphamvu kamodzi.
Timuyi idakwanitsa kugoletsa zigoli zitatu m’masewero onse pomwe Burkina Faso idamwetsa zigoli zisanu ndi ziwiri.
Timuyi ili mu Gulu B momwe muli Uganda, Burkina Faso ndi South Sudan.
Flames ndiyachitatu mu gululi ndi mapointi atatu pomwe Uganda ndi Burkina Faso ali ndi mapointi anayi. South Sudan ilibe pointi.
M’masewero am’mbuyomu Flames idagonjetsa South Sudan 1 kwa duu koma idagonja 2 kwa duu ndi Uganda. Matimu awiri oyambirira ndiomwe akapikisane nawo kun dime yomaliza ya AFCON.