MkwasoUncategorized

‘Ufulu wa amayi povota ulemekezedwe’

Amayi ngati awa amaponya voti

Mlandu wa chisankho cha Pulezidenti cha pa 21 Meyi unabweretsa mbali zingapo zokhudzidwa monga zipani za ndale, bungwe la chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) ndi abwenzi akhoti monga la maloya achizimayi la Women Lawyers Association, lomwe omwe adaliyimira pa mlanduwu ndi a Bernadette Malunga. Nchifukwa chiyani bungweli lidalowa mlanduwu ngati abwenzi akhothi? Zolinga za bungweli ndi zotani? A Malunga adacheza ndi GODFREY MAOTCHA pa nkhanizi ndi zina.

Tiuzeni mbiri yanu?

Ndimagwira ntchito ku koleji ya Chancellor, ku nthambi yophunzitsa malamulo. Ndili ndi digiri ya udotolo wa zamalamulo komanso ndinachita za ukadaulo (Masters) zokhudza amayi pa malamulo motero nkhani ya amayi ndi mbali yanga. Ndimachokera kwa Mfumu Yaikulu mwambo m’mudzi mwa Kumisuku m’boma la Zomba.

Malunga: Tikulimbikitsa ufulu wa amayi poponya voti

Bungweli lidayamba liti ndipo ndi zolinga zanji?

Bungweli lidayamba cha m’ma 1998 ndipo cholinga chake chinali kumenyera ufulu amayi ndi ana. Ife timapereka mwayi woimira mlandu kwa amayi monga upangiri komanso kuimira amayiwa pa mlandu.

Mumachita chiyani kuti mulimbikitse atsikana kulowa ntchito ya za malamulo?

Kwenikweni osati kuchokera ku bungwe lathu. Koma Yunivesite ya Malawi ndi bungwe la National Council for Higher Education (NCHE) amadziwitsa ophunzira za maphunziro omwe akupezeka mu sukulu za ukachenjede. Apa ndi pomwe iwo akufuna kuti ophunzirawa akayambe maphunziro awo. Nthambi ya za malamulo ku Yunivesiteyi imakopa ophunzira kuphatikiza atsikana.

Munganenepo chiyani pa za chiwe-rengero cha amayi pa ntchito yoimira milandu?

Amayi ndi ochepa komabe tikuyesetsa. Ndithudi ntchito tili nayo kuti tichulukitse chiwerengero cha amayiwa pa ntchitoyi.

Mwa anthu asanu oweruza mlandu wa chisankho, mayi ndi mmodzi. Zimenezi sizikukukhudzani?

Sindikudziwa zomwe ankayang’ana posankha oweruza mlanduwu.Tikadakonda kuti pa gululi pakhale amayi angapo koma mwina pali zifukwa zomwe zidakhalira chonchi. Mwina ena adatanganidwa kapena samapezeka. Vuto ndi lomwe lija kuti amayi ndi ochepa mu ntchito za malamulo. Nako ku nthambi yoweruza milandu majaji achizimayi ndi ochepa kwambiri.

Pali njira yapadera yomwe bungwe lanu limatsata poimira amayi pa mlandu?

Izo ndiye zomwe timapanga. Amayi omwe alibe kuthekera timawathandiza kuwaimira m’mabwalo a milandu ngati taona kuti tili ndi kuthekera kutero.

Nanga pali njira zakuti atsikana ochuluka azitengedwa kukaphunzira za malamulo mu sukulu zaukachenjede?

Sukuluzi zimapemphedwa kutero kudzera mu lamulo la kusasiyana pakati pa amuna ndi akazi. Apa ndiye kuti malire 60 peresenti ya amuna kapena akazi komanso osachepera 40 peresenti ya amuna kapena akazi. Zimenezi zimachitika pa nthambi ya za phu-nziro lomwe likuphunzitsidwa pa sukulupo. Apa tikutanthauza kuti zotere zimatengera ngati munthu wakhonza mayeso olowera ku nthambiyi. Sungatenge munthu yemwe walephera mayeso pongotengera kuti ndi mkazi kapena mwamuna.

Mwati kuponya voti ndi ufulu wa chibadwidwe wa amayi komanso munthu. Tafotokozani bwino?

Ufulu woponya voti ndi ufulu wa anthu. Ife tikulimbikitsa ufulu wa amayi poponya voti. Ambiri omwe adaponya voti ndi amayi choncho liwu la anthu ochuluka omwe ndi amayi limveredwe. Ngati chisankho sichidayende bwino zitha kukhudza amayi omwe adaponya voti. Chimodzimodzi ngati chisankhochi chidayenda bwino.

Pali nkhani yokhudza mtopola omwe amayi ndi asungwana adachitiridwa kwa Msundwe, Mpingu ndi Mbwatalika m’boma la Lilongwe. Mukuchitapo chiyani pa nkhaniyi?

Tapempha apolisi kuti aike nthambi yoima payokha kuti ifufuze za mtopolazi, ndipo tapita kwa Msundwe kukaphunzitsa amayi ndi asungwana za ufulu wawo ndiponso momwe lamulo lingawathandizire.

Mawu anu omaliza ndiotani?

Ufulu wa amayi ndi mbali imodzi ya ufulu wa chibadwidwe. Ife monga maloya a chizimayi timafuna anthu ambiri ogwira nafe ntchito poli-mbikitsa maufulu a amayi ndi  atsikana. Tikatero ndiye kuti tizatukula dziko la Malawi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *