MkwasoNkhani Zina

Abambo yankhulani za kukhosi — Men’s Voices

Wolemba: Watipaso CHIBWANA, Mtolankhani Wapadera

Bungwe la Men’s Voices lapempha abambo m’dziko muno kuti adzitula nkhawa zawo kwa amnzawo kape-nanso achibale komanso mabungwe osiyanasiyana ngati njira imodzi yochepetsera chiwerengero cha abambo ambiri amene akudzikhweza m’dziko muno.

Mkulu wa bungweli, lomwe lili ku Zomba, a Taona Steven Mkandawire, ndiwomwe apereka pempholi kutsatira lipoti la apolisi laposachedwapa lomwe latuluka mwezi wa Novembela lomwe linati anthu 482 ndiomwe adzipha okha kuyambira mu mwezi wa Januwale mpaka Seputembala chaka chino chokha.

Ndipo mwa anthu 482, amuna omwe adzipha okha ndi 415 pamene amayi ndi 67; zomwe a Mkandawire ati ndi zodandaulitsa kwambiri pa chitukuko cha dziko.

Iwo anati abambo ambiri akukumana ndi nkhanza zambiri m’banja koma vuto samabwera poyera kuti anene zomwe zili kukhosi kwawo ndiye zikawatopetsa amangoganiza zokazipha ngati njira yothanirana ndi vutolo.

Mkuluyu anapitiriza kunena kuti zifukwa zazikulu zomwe zimapangitsa abambo ambiri kudzipha ndi nkhani za ngongole komanso za m’banja.

Mwachitsanzo a Mkandawire anati abambo ambiri akakhala ndi ngongole yochuluka ndipo akawona kuti sakwanitsa kuyibweza amalingalira zokazipha.

Kuphatikiza apo, iwo anatinso abambo ambiri akadziwa kuti mkazi wawo ali paubwenzi wamseli ndi mwamuna wina ndipo apeza u-mboni onse, amakangozimangirira posafuna kuwoneka wopepera.

Mkandawire: Chiwerengero cha amuna amene akuzipha chikuchititsa mantha (Photo Credit: Watipaso Chibwana)

Apa a Mkandawire anatsindika kuti pakufunika uphungu komanso maphunziro okwanira kuti abambo azindikire za udindo omwe alinawo ku banja lawo asanalingalire zokazipha.

Malingana ndi a Mkandawire, nawonso akuti mkazi wawo wa kale anachitapo maubwenzi ndi amuna zomwe zinawapangitsa kusiyana nawo koma adazibweza ku lingaliro lodzipha ataona kuti ana awo adzavutika popanda iwowo.

Mkuluyu anapitiriza kunena kuti ndi chifukwa chake analingalira zokhadzikitsa bungwe lawo la Men’s Voices kuti adzifikira abambo ambiri ndi uthenga woletsa kudzipha pakati pawo kuti chiwerengero chodzipha chichepe m’dziko muno.

“Ndipemphe kuti chonde abambo tiziyankhula za kukhosi ndi amnzathu chifukwa tikatero timapepukidwa kutsatira uphungu womwe amnzathu amatipatsa. Nthawi yodzipha inatha, tiyeni tivomereze zikachitika ndikupita chitsogolo ndi moyo wathu,”anatero a Mkandawire.

A Chiwoza Bandawe, womwe ndi dotolo wamkulu pa nkhani za malingaliro angwiro m’dziko muno, anauza Zodiak Online pa 8 Nove-mbela chaka chino kuti pakufunika kukhazikitsa mabungwe a abambo ochuluka komwe azikakambiranako zomwe zikuwapsinja ndi kupepukidwa ku nkhawa zawo.

Iwo anauzanso MBC Online posachedwapa kuti ndiwokhutira tsopano ndi kukhazikitsidwa kwa bungwe la Men’s Voices kaamba koti lithandizirako kuchepetsa imfa zobwera kaamba kozimangilira pakati pa abambo.

Mikangano ya m’banja ikupangisanso kuti abambo ambiri azidzikhweza (Photo Credit: Internet)

Mwazina, bungweli lizichititsa masewero osiyanasiyana m’malo ambiri omwe abambo amapezekerako monga ku mowa kuti pamene matimu akulimbirana ndalama posewera masewero, kumbali inayi azimwaza uthenga wokhudzana ndi kudziletsa ku mchitidwe wodzipha.

Ambiri mwa mamembala omwe ali mu bungweli ndi abambo omwe anakumanapo ndi nkhanza ndi akazi awo ndipo anapulumuka ku lingaliro lofuna kudzipha okha atamasukirana ndi amnzawo.

Pakadali pano, bungweli likupempha akufuna kwabwino kuti alithandize ndi thandizo lina lili-lonse ndicholinga choti lithe kufikira abambo ochuluka m’dziko muno pa nkhani zangati zomwezi ndipo ofuna kuyankhulana ndi mkulu wa bungweli atha kuwapeza pa manambala awa: 0991 370 388 kapena 0888 872 931.