CHIPWIRIKITI KU CDF
Chilima wati katemera ‘si zasataniki’
Wolemba:
Chikumbutso MANG’ANDA
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Saulos Klaus Chilima wati walimbikitsa anthu kuti apite kukabayitsa katemera wa matenda a Covid-19 ponena kuti katemerayu si nkhani za ‘sataniki’. Dr Chilima amalankhula zimenezi ku Mzuzu atalandira katemera wa Astrazeneca potsegulira ntchito yobayitsa katemerayo.“Omwe akukamba zosayenera zokhudza katemerayu ndi atumiki asatana,” anatero a Chilima.
A Chilima anakumbutsa anthu kufunika kopitiriza kutsatira njira zopewera kufala kwa matendawa. “Ndafuna kutengeraposo mwayi pa mwambowu kukumbutsa Amalawi kuti kulandira katemera sikukutathauza kuti mliriwu watha pakati pathu ayi,” anatero a Chilima. Naye mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera ndi mkazi wake anali oyambirira kulandira katemerayu ku Zomba. Dziko lino linalandira katemera wokwanira 360 sauzande yemwe ataperekedwe kwa anthu osiyanasiyana maka anthu omwe amagwira ntchito ku chipatala komanso omwe ali ndi matenda ena am’gonagona monga chifuwa chachikulu cha TB. Dziko la Malawi linalandira katemerayu kuchokera
ku bungwe loonetsetsa kuti maiko omwe ndiovutika akupeza nawo katemerayu la Covax. Munthu akuyenera kulandira katemerayu kawiri
pakatha sabata pafupifupi zisanu ndi ziwiri.
Zala ziloza aphungu
Pamene nkhani zakusakazika kwa ndalama za thumba la chitukuko chakudera la aphungu za Constituency Development Fund (CDF)
zikupitirira kumveka, zala zonse zikulodza aphungu kuti ndiamene akusakaza ndalamazi pozigwiritsa ntchito mu njira zosayenera. Chaka chilichonse boma limapereka K40 miliyoni kudera lirilonse la phungu imene imabwera m’magawo angapo. Pa ndalama imeneyi pamakhala K8 miliyoni yothandizira
ophunzira osaukitsitsa kuwalipilira sukulu fizi ndipo ina imakhala yoti ichitire zitukuko zakudera. Ndalamazi, zomwe zimafikira ku khonsolo, amazilamulira ndi phungu pochitira zitukuko. Malinga ndi ndondomeko ya CDF, anthu akumudzi akuyenera kumatenga nawo mbali posankha chitukuko ndi kulondoloza m’mene ntchito yachitukuko ikuyendera. Koma zaonetsa kuti aphungu ambiri salabada zogwira ntchito limodzi ndi anthu akumudziwa zomwe zikupangitsa kuti aphungu azisakaza ndalamazi pantchito zao. Nthawi zina ati aphungu amakauza a ku khonsolo kuti awapatse ndalama
zokalipira ntchito ya chitukuko chonsecho palibe chomwe chachitika. Yemwe nthawiyo anali bwanamkubwa wa boma la Mulanje a Charles Makanga anati thumba la CDF ndi lovuta kuti aku khonsolo alilondole ndipo mabwanamkubwa alibe mphamvu potengera m’mene thumbali limayendetsedwera.
“Pa pepala, bwamkubwa ali ndi mphamvu, koma zoona zenizeni iye alibiretu mphamvu malinga ndi m’mene thumbali limayendetsedwera,”
anatero a Makanga pouza Nyasatimes. Phungu wadera lapakati pa boma la Machinga a Samuel Malume Bokosi anati sizoona kuti aphungu amakhala ndi mphamvu yambiri pa ndalama za CDF koma makomiti achitukuko amasankha chitukuko
chomwe akufuna. “Makomiti achitukuko amakhala ndi zomwe akufuna kuti tichite. Mphamvu yanga ndiyosayinira chitukuko chomwe tagwirizana kuti
akhonsolo atipatse ndalama osati ineyo kulamula khonsolo kundipatsa ndalama kukapangira zina ayi,” anatero a Bokosi. A Bokosi anaonjezera kuti: “Ngati pali aphungu omwe akumanama chitukuko chomwe alandira kudera kuchokera kwa amabungwe ndi anthu akufuna kwabwino kunamizira kuti
agwiritsa ntchito ndalamayi ndi zolakwika chifukwa pano anthu akumudzi akuchita kaolondolondo wa zitukuko okha ndipo ngati pali mavuto amatha
kunena pomwe awona zachinyengo.” Phungu wakale wadera la kumadzulo kwa boma la Balaka a Patricia Shanil Dzimbiri anati munthawi yao phungu samakhala ndi mphamvu yolamula ogwira ntchito ku khonsolo kuwapatsa ndalamayi kuti akagwiritse ntchito. “Ntchito yanga inali kulondoloza
chitukuko ndi kusayina chikalata chokhudza zitukuko zomwe anthu agwirizana ndi kuvomereza kuti tipange osati kuzichitira ndekha popanda kuwadziwitsa mafumu ndi makomiti achitukuko,” anatero a Dzimbiri.
A Dzimbiri anati palibe chitukuko chomwe anachita kudumpha makomiti achitukuko kapena khonsolo osadziwa. “Kukasankhidwa chitukuko monga
kumanga milatho, kukumba mijigo ndi zina mkulu woona za chitukuko ku khonsolo amadzayendera ndi kuwona ngati ndalama yomwe yabwera ikwanire
osati kukangowawuza kuti andipatse ndalama ndikagwiritse ntchito. Ndimakhulupirira kupanga zinthu poyera osati kuchita kumbali,” anatero a
Dzimbiri. Katswiri pankhani zaulamuliro wabwino a Henry Chingaipe anati sangayankhulepo kanthu chifukwa anapereka kale maganizo awo pa momwe thumba la CDF liyenera kugwirira ntchito. “Ine mogwirizana ndi bungwe la CCJP [Catholic Commission for Justice and Peace] tinapanga kale mlozo wa
momwe thumbali liyenera kumayendera ndipo Unduna wa Zamaboma aang’ono unavomerezanso mlozowo koma vuto ndi aphungu omwe sakufuna
kuvomereza ndondomekozo,” anatero a Chingaipe. A Chingaipe anati kafukufuku yemwe anachita, anapeza kuti thumba la CDF silikugwiritsidwa bwino ntchito ndipo kuti aphungu ambiri amagwiritsa mphamvu zao molakwika pomawaopseza a ku khonsolo akafuna kutenga ndalamazi. Kafukufuku yemwe bungwe la CCJP lachita posachedwapa m’maboma asanu ndi limodzi wa m’mene ndalama zimagwiritsidwira ntchito m’makhonsolo pa zitukuko waonetsa
kuti thumba la CDF silimagwiritsidwa bwino ntchito ndipo ndalama zomwe zimalembedwa zimakhala zosemphana ndi zomwe zagwira ntchito. Mmodzi mwa akuluakulu ku bungwe la CCJP a Lawrence Valens Khoriyo anati apeza kuti pa zitukuko zomwe zinachitika mu 2019 ndi
2020 m’madera a aphunguwa sizinayende bwino. “Mwa chitsanzo ntchito yoyika magetsi yomwe inachitika pa chipatala chaching’ono cha Mwima [m’boma la Balaka] anati anagwiritsa ntchito K5.5 miliyoni koma titakawona ndi zipangizo zomwe anagwiritsa ntchito ndalamayi ndiyochuluka kwambiri.
Palinso zitukuko zina zomwe ndalama zomwe zikunenedwa ndi ntchito yake ndi zosagwirizana,” anatero a Khoriyo. Boma la Malawi lidayambitsa
thumba la CDF m’chaka cha 2006 kuti lizithandizira pa ntchito zachitukuko m’madera a aphungu. Maiko pafupifupi 23 ndiamene akugwiritsa ntchito ndondomeko ya CDF. Muno mu Africa, CDF ili m’maiko monga Ghana, Kenya, Malawi, Liberia,Rwanda ndi Zambia.