Malume Bokosi atulutsa yolawitsa
Wolemba: Bartholomew BOAZ
Atakhala zaka zisanu ndi zi- wiri asakumveka, mkhalakale pa zoimba Malume Bokosi walengeza kubwereranso ndi nyimbo ya kalawe yotchedwa ‘Muwalange’ yomwe ituluke mwezi wa February chaka chino.
Bokosi adatulutsa komaliza chimbale chotchedwa ‘Wakukhoti’ m’chaka cha 2010. Chitulutsireni chimbalecho, iye adazimilira os- amvekanso.
“Bokosi adakalipo, Amalawi ayembekezere kumvera nyimbo yat- sopano yabwino,” anatero Bokosi.
Iye anati kupatula ‘Muwalange’ yomwe yangotsala pang’ono kutha kujambula, akufuna kutulutsanso ny- imbo zina zinayi kenako azijambule nyimbozo m’ chimbale choonera chotchedwa ‘Malawi Wanga’.
“Ndikufuna kujambula nyimbo zimenezo kuti ndiwakumbutse Amalawi kuti ndidakalipo. Anthu ambiri amene amandikonda akhala akudandaula kuti andisowa ndipo
akufunisitsa kuti ndidziimbabe. Ndi- panga kufuna kwao.”
Bokosi adatchuka m’ chaka cha 2001 ndi chimbale cha ‘Alimi Tidalakwanji’ . M’ chaka cha 2004 adatulutsanso ‘Kukamwa Kwa- ngotiuma’ , ‘Malaulo Samapemphe- dwa’ (2006), ‘Penshoni’ (2008) kenako ‘Wakukhoti’. ‘Kukamwa Kwangotiuma’ ndi chimbale cho- mwe chidagulitsa kwambiri.
“Sikuti pakhala kusiyana kwambiri pa maimbidwe anga. Ndi- imba monga momwe anthu ama- ndidziwira,” anatero Bokosi yemwe nyimbo zake monga ‘Wakana Kukayezetsa’ ndi ‘Akuvulalira M’ kati’ zinatenga malo m’ mbu- yomu.
Padakali pano, Bokosi waulu- lanso malingaliro ake ofuna kudza- pikisana nawo pa mpando wa phungu wadera lapakati la boma la Machinga pa chisankho cha chaka chamawa.
Iye wati adzaimira chipani cho- lamula cha Democratic Progressive (DPP) pomwe adzapikisane ndi phungu wa derali a Shaibu Kaliati (United Democratic Front – UDF), Mbusa Rex Chitekwe ndi mayi Khembo (awiriwa oima paokha).
Thanks for sharing. I read many of your blog posts, cool, your blog is very good.