Wokomaatani Malunga akhazikitsa mabuku atatu a ndakatulo
Wolemba: Joseph Kayira
Katswiri komanso mkhalakale pa nkhani ya zolembalemba, a Benedicto Wokomaatani Malunga, Lamulungu pa 6 Sepitembala 2026 anakhazikitsa mabuku awo a ndakatulo atatu pa mwambo womwe unachitikira ku sukulu yaukachenjede ya DMI – St John the Baptist ku Mangochi.
Mabukuwa, omwe alembedwa mu chilankhulo cha Chinyanja ndi Chingerezi ndi ‘Nasiwelo ndi Ndakatulo Zina’, ‘Taming the State of Mind’ ndi ‘Writing Odyssey’. Ndakatulozi zalembedwa mwakuya ndi mozamitsa chikhalidwe cha chimalawi, malingana ndi a Malunga.

Mlendo wolemekezeka, a Namalomba kudzanso a Malunga ndi alendo ena, kuyendera malo omwe a Montfort Media amagulitsa mabuku awo
Polankhula pa mwambowo, a Malunga anati ndi wokondwa kuti ndakatulo zomwe azilemba mwakuyazi, ziphunzitsa komanso kusangalatsa Amalawi ndi ena onse amene amasangalatsidwa ndi ndakatulo zawo.
Iwo anati mabuku atatuwa anawalemba atalingalira mozama za luso lawo ndipo akukhulupirira kuti athandiza pa nkhani ya chikhalidwe, maphunziro ndi msangulutso.
“Kulemba ndakatulo ndi nkhani zina zimene zimasintha kapena kuphunzitsa anthu nkofunikira kwambiri; kuwerenga ndi kofunikiranso kwambiri. Kulembaku kumathandiza kuti tiike malingaliro athu mu chinthu chooneka – ngati m’mene tachitira ndi mabukuwa. Ndikupempha Amalawi ndi ena onse kuti agule ndi kuwerenga mabukuwa; agawane mabukuwa; awaike mu nyumba zosungira mabuku komanso athe kukambirana za luso limeneli,” anatero a Malunga.

A Malunga (kumanja) kupereka buku kwa mlendo wolemekezeka, a Namalomba
Iwo anayamikiranso sukulu ya ukachenjede ya DMI – St John the Baptist polola kuti mwambowo uchitikire pa sukuluyo zomwe zikugwirizana ndi malingaliro oti mabukuwa azipezekanso mu sukulu za ukachenjede kuti ophunzira athe kukhala ndi mpata wophunziranso luso pa kalembedwe.
A Malunga, omwe akhala akulemba ndakatulo zawo zambiri mu chilankhulo cha chinyanja, akuti ulendo uno anaganiza zolemba ndakatulo zina mchingerezi kaamba koti palinso anthu ena amene amafuna atamalondola luso lawo kudzera mchilankhulochi.
“Izi sizikutanthauza kuti ndisintha kalembedwe kanga ka ndakatulo kamene mumakadziwa kaja ayi. Ndachita izi pofuna kufikira anthu amene amakonda kalembedwe kanga pa za msangulutso koma chilankhulo cha chinyanja samachimvetsa bwino. Pokhala kuti tili m’dziko limene muli anthu a mitundu yosiyanasiyana, kuwafikira anthu olankhula ziyankhulo zina ndi kwabwinonso,” anatero a Malunga.

Bambo Jailosi: Kampani ya Montfort Media inasindikiza limodzi mwa mabukuwa
Iwo anaululanso maloto awo kuti pakali pano akulingalira zozatanthuzira mabuku awiri kuchokera mchingerezi kupita mchinyanja ndipo mabukuwa ndi ‘Julius Caesar’ lolembedwa ndi William Shakespeare komanso ‘Cry My Beloved Country’ lolembedwa ndi Alan Paton.

Ili ndi limodzi mwa mabuku omwe a Malunga alemba ndi kukhazikitsa
Nduna yofalitsa nkhani, yomwenso inali mlendo wolemekezeka, a Shadreck Namalomba, anayamikira a Malunga chifukwa cha luso lolemba ndakatulo zomwe zakhala zikusangalatsa anthu kwa zaka zambiri. Iwo anati a Malunga ali ngati mphatso ku dziko la Malawi kaamba ka luso lawo lolemba.
“Ntchito imene ationetsa kudzera m’mabuku atatuwa ndi yapamwamba kwambiri ndipo ikuyenera kulemekezedwa, kutamandidwa komanso kulimbikitsidwa. Ndili ndi chikhulupiriro kuti izi zilimbikitsanso anthu kukhala ndi chidwi chowerenga mabuku,” anatero a Namalomba.

A Namalomba akuti boma likuchita chotheka kuti aluso nawo azisangalala
Ndunayi inati boma likulimbikitsa luso losiyanasiyana ndipo ichi nchifukwa lidakhazikitsa bungwe la Copyright Society of Malawi (COSOMA) kuti lizithandiza aluso osiyanasiyana, kuphatikizapo luso lolemba, kuti azipindula ndi luso lawolo.
“Chofunika ndi choti aluso onse alembetse mkaundula wa COSOMA kuti athe kupeza kangachepe kudzera mu luso lawo. Boma likuchita chotheka kuti luso la oimba, olemba mabuku ndi ena, lithenso kuwapindulira. Pali zambiri zimene tikuchita ngati boma kuti aluso asatsalire m’mbuyo koma kuti tiyendere limodzi,” anatero a Namalomba.
Bambo Blaise Jailosi, omwe ndi mkulu woyendetsa kampani ya Montfort Media, yomwe inasindikiza limodzi mwa mabukuwa, la ‘Nasiwelo ndi Ndakatulo Zina’, anati ndi zosangalatsa kuti maloto a Malunga atheka kudzera mu kusindikiza mabukuwa.

Woimba Agorosso naye anali konko kusangalatsa anthu
Iwo anapempha anthu kuti athandize kutukula luso la a Malunga pogula mabukuwo. Bambo Jailosi anati mabukuwa ndi apamwamba ndipo ndikofunika kuti anthu amene amakonda kuwerenga agule ndi kulemekeza luso limene a Malunga awonetsa.
Pa mwambo wokhazikitsa mabukuwo, buku la ‘Nasiwelo ndi Ndakatulo Zina’ ndi la ‘Taming the State of Mind’ anagulitsidwa pa mtengo wa okushoni wa K500,000 lililonse ndipo buku la ‘Writing Odyssey’ linagulidwa pa mtengo wa K350,000.
