NICE ilalika za mtendere
Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA
Bungwe lophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana la National Initiative and Civic Education (NICE) Trust lapempha anthu m’dziko muno kuti asunge bata ndi mte-ndere pamene akudikira zotsatira za mlandu wa chisankho ndipo kuti zikadzaulu-tsidwa pasadzakhale ziwawa.
Mkulu woona ntchito za bungweli a Enock Chinkuntha amalankhula izi m’boma la Balaka komwe bungweli limazindikiritsa anthu am’derali mmene nthambi za boma zimayenera kugwirira ntchito zake komanso thandizo lomwe anthu amayenera kupeza pa zipatala zomwe zili m’dera lawo.
Iwo anati mmene nkhani ili ku khothi anthu otsatira zipani zosiyanasiyana apewe ziwawa komanso kuchita chisokonezo mlanduwu ukatha.
“Tikudziwa tonse kuti nkhani yokhudza chisankho ili ku khothi ndipo nkhaniyi akapereka chigamulo ena chidzawakomera [ndipo] ena ayi. Chonde tiyeni tidzapewe mchitidwe womwe udzadzetse ziwawa koma kuvomereza zomwe zabwera posatengera chipani chomwe tili ndi kuti chitukuko chipitirire kuyenda bwino m’dziko muno,” anatero a Chinkuntha.
A Chinkuntha anati nkhaniyi ikatha pakuyenera kukhala bata komanso onse osangalala asadzasa-ngalale mopyola muyezo kuti ena adzamve kuwawa ndi kuyambitsa ziwawa.
“Mudzasangalale mosaphera ena ufulu, ndipo omwe sizidzawakomera asadzawonetse mkwiyo wawo pobwezera ndi ziwawa,” anatero a Chinkuntha.