Nyerere zanyotsola Maule
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yadyetsedwa mpunga wa miyala ndi timu ya Mighty Wanderers lero pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre itagonja ndi chigoli chimodzi kwa ndanda mu chikho cha TNM Supa Ligi.
Chigoli chomwe anagoletsa mnyamata Blessings Mwalilino pa mphindi 11′ za masewerowa chinali chokwanira kuti Manoma alize gulu lochuluka lomwe linatsatira Maule ku bwaloli.
Ngakhale timuyi yagonja, iyo yakhalabe patsogolo pa mndandanda wa matimu mu ligiyo ndi ma pointi 18 pa masewero asanu ndi awiri ndipo Manoma ali pa nambala yachiwiri ndi mapointi 16 atasewera masewero asanu ndi amodzi.
Manoma agwetsa Maule koyamba kuyambira 2021 m’masewero a ligiyi ndipo aka nkoyamba Bullets kugonja mu ligiyi.