MkwasoZa M'dziko

‘Aliyense ali ndi udindo woteteza zipangizo za madzi’

Wolemba: Edwin GAWANI, Mtolankhani Wapadera

Nthambi ya madzi mu mzinda wa Lilongwe ya Lilongwe Water Board (LWB) yati ndi udindo wa aliyense kuwonesetsa kuti zipangizo za madzi zikutetezedwa kwa a mbanda poyika ndondomeko zabwino m’madera mwawo.

Wogwirizira udindo wa wamkulu wa nthambiyi a Maclean Nyang’wa ndiwomwe anayankhula izi kutsatira kuchilimika kwa anthu a m’dera la Chinsapo mu mzindawu amene anagwira mnyamata wina yemwe anaba ma mita komanso mipopi ya madzi.

“Aliyense ali ndi udindo wowonesetsa kuti zipangizo za madzi zikutetezedwa mokwanira mu madera athu omwe tikukhala. Makasitomala akuyenera kuyika ndondomeko zabwino zothandiza kuwonesetsa kuti ma mita ndi zipangizo zina ndizotetezedwa bwino,” anatero a Nyang’wa.

Wina mwa katundu yemwe anapezeka ndi wakubayo (Chithunzi: Facebook)

Choncho iwo anayamikra ena mwa anthu okhala m’dera la Chinsapo chifukwa chodzipereka powo-nesetsa kuti mmodzi mwa anthu amene amawononga katundu wa bungweli agwidwe ndi kuperekedwa ku polisi.

Iwo anati zomwe anachita anthuwa ndi chitsanzo chabwino cha umodzi pakati pa anthu komanso zilinganizo zawo mogwirizana ndi apolisi zowonesetsa kuti zipangizo za madzi zikutetezedwa m’madera osiyanasiyana.

Malingana ndi uthenga wa bungweli pa tsamba lake la Facebook, anthu ena kwa Chinsapo anaona mnyamatayu ali ndi ma mita a madzi komanso mipopi yomwe anakayikira kuti yachotsedwa m’makomo mwa anthu osiyanasiyana. Bungweli linati apa ndipomwe anthuwo anaganiza zomugwira ndikumupititsa ku polisi.

Kubedwa komanso kuwononga mwadala zipangizo za mabungwe operekera madzi ndi gwero limodzi lomwe mabungwewa amati zimakhudza ntchito yawo yoperekera bwino madzi.